Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mawu Ofotokoza Chigawo cha 9

Mawu Ofotokoza Chigawo cha 9

Chigawochi chikufotokoza za achinyamata, aneneri komanso mafumu amene anasonyeza kuti ankakhulupirira kwambiri Yehova. Ku Siriya kunali kamtsikana kena ka ku Isiraeli komwe kankakhulupirira kuti mneneri wa Yehova angathe kuchiritsa Namani. Mneneri Elisa ankakhulupirira kuti Yehova angamupulumutse kwa adani ake. Mkulu wa Ansembe dzina lake Yehoyada anaika moyo wake pangozi kuti apulumutse Yehoasi amene agogo ake a Ataliya ankafuna kumupha. Mfumu Hezekiya inkakhulupirira kuti Yehova apulumutsa Yerusalemu ndipo sanagonjere zimene Asuri ankafuna. Mfumu Yosiya inachotsa mafano, kumanganso kachisi n’kuthandiza anthu kuti ayambirenso kulambira koona.

M'CHIGAWO ICHI

MUTU 51

Kamtsikana Kanathandiza Mkulu wa Asilikali

Kamtsikana kachiisiraeli kanauza abwana ake aakazi kuti Yehova ali ndi mphamvu zochiritsa.

MUTU 52

Gulu Lamphamvu la Asilikali a Yehova

Kodi mtumiki wa Elisa anadziwa bwanji kuti ‘panali ambiri amene anali kumbali yawo kuposa amene anali kumbali ya adani awo’?

MUTU 53

Yehoyada Anali Wolimba Mtima

Wansembe wokhulupirika analimbana ndi mfumukazi yoipa.

MUTU 54

Yehova Anamulezera Mtima Yona

Kodi zinatani kuti mneneri wina wa Mulungu amezedwe ndi chinsomba? Nanga anatuluka bwanji m’mimba mwa chinsombacho? Kodi Yehova anamuphunzitsa chiyani?

MUTU 55

Mngelo wa Yehova anateteza Hezekiya

Adani a Ayuda ankanena kuti Yehova sangathandize anthu ake, koma zimenezi sizinali zoona.

MUTU 56

Yosiya Ankakonda Chilamulo cha Mulungu

Yosiya anakhala mfumu ya Ayuda ali ndi zaka 8, ndipo anathandiza anthu ake kuti azilambira Yehova.