Yehosafati anali mfumu ya Yuda ndipo anagumula malo operekera nsembe a Baala komanso anawononga mafano onse m’dzikolo. Yehosafati ankafuna kuti anthu adziwe malamulo a Yehova. Choncho anatumiza akalonga ndi Alevi kuti akaphunzitse anthu malamulo a Yehova mu Yuda monse.

Anthu a m’mayiko oyandikana ndi Ayuda ankaopa kuwaukira chifukwa ankadziwa kuti Yehova ali nawo. Anthuwo mpaka ankapereka mphatso kwa Mfumu Yehosafati. Koma Amowabu, Aamoni ndi anthu ochokera ku Seiri anabwera kuti adzamenyane ndi Ayuda. Apa Yehosafati anadziwiratu kuti akufunika kuthandizidwa ndi Yehova. Zitatero anaitanitsa amuna, akazi ndi ana kuti abwere ku Yerusalemu. Anthuwo atafika, iye anapemphera kuti: ‘Yehova, popanda inu sitingapambane nkhondoyi. Chonde tithandizeni chifukwa sitikudziwa chochita.’

Yehova anayankha pempherolo kuti: ‘Musaope chifukwa ndikuthandizani. Khalani m’malo anu, imani chilili ndi kuona ndikukupulumutsani.’ Kodi Yehova anawathandiza bwanji?

Tsiku lotsatira, Yehosafati anasankha anthu oimba n’kuwauza kuti aziyenda patsogolo pa asilikali. Anthuwo anayenda kuchokera ku Yerusalemu mpaka ku Tekowa komwe kunachitikira nkhondoyo.

Iwo ankaimbira Yehova mokweza ndipo iye anamenyera nkhondo anthu ake. Anachititsa kuti Amowabu ndi Aamoni ayambe kuphana okhaokha ndipo palibe amene anapulumuka. Yehova anateteza Ayuda asilikali komanso ansembe. Anthu a m’mayiko oyandikana ndi Ayuda anamva zimene Yehova anachitazi ndipo anadziwa kuti iye akuthandizabe anthu ake. Kodi Yehova amapulumutsa bwanji anthu ake? Amawapulumutsa m’njira zosiyanasiyana ndipo safunika kuthandizidwa ndi anthu kuti achite zimenezi.

“Simufunikira kumenya nkhondo. Khalani m’malo anu, imani chilili ndi kuona Yehova akukupulumutsani.”​—2 Mbiri 20:17