Yehova anadalitsa Solomo pomupatsa nzeru komanso mwayi woti adzamange kachisi. Koma patapita nthawi Solomo anasiya kulambira Yehova. Ngati ndinu kholo, fotokozerani mwana wanu zimene zinachititsa kuti Solomo asiye kulambira Yehova. Ufumu wa Isiraeli unagawikana ndipo mafumu oipa anachititsa kuti anthu asiye kulambira Mulungu n’kumalambira mafano. Pa nthawi imeneyo, atumiki ambiri a Yehova ankazunzidwa kapenanso kuphedwa kumene. Mfumukazi Yezebeli inachititsa kuti anthu a mu ufumu wakumpoto azilambira kwambiri mafano. Imeneyi inali nthawi yovuta kwambiri kwa Aisiraeli. Komabe panali anthu ena amene ankatumikira Yehova mokhulupirika. Ena mwa anthuwa anali Mfumu Yehosafati komanso mneneri Eliya.