Sauli atafa, Davide anakhala mfumu. Iye anayamba kulamulira ali ndi zaka 30. Tsiku lina ali padenga la nyumba yake anaona mkazi wokongola. Atafufuza anapeza kuti dzina lake anali Bati-seba ndipo anali mkazi wa Uriya. Davide anaitanitsa mkaziyo ndipo anagona naye. Atazindikira kuti mkaziyo ali ndi mimba, Davide anapeza njira yoti tchimo lakelo lisadziwike. Iye anauza mkulu wa asilikali kuti aike Uriya kutsogolo n’kumusiya kuti aphedwe. Izi zinachitikadi ndipo Davide anakwatira Bati-seba.

Koma Yehova ankaona zonsezi. Kodi ndiye anatani? Iye anatumiza Natani kuti akakambirane ndi Davide za nkhaniyi. Natani atafika kwa Davide anamuuza kuti: ‘Panali munthu wina wolemera amene anali ndi nkhosa zambiri ndiye panalinso wosauka yemwe anali ndi kankhosa kamodzi kokha. Wosaukayo ankakakonda kwambiri kankhosa kakeko. Ndiyeno munthu wolemera uja analanda kankhosa ka wosaukayo kuti kakhalenso kake.’ Davide atamva zimenezi, anakwiya kwambiri ndipo anati: ‘Munthu ameneyo ayenera kufa basi.’ Natani anauza Davide kuti: ‘Munthu wolemerayo ndi inuyo.’ Davide anazindikira zimene Natani ankatanthauza ndipo anamva chisoni. Ndiyeno anauza Natani kuti: ‘Ndachimwira Yehova.’ Tchimo limeneli linam’bweretsera mavuto Davide limodzi ndi banja lake. Yehova anapereka chilango kwa Davide koma sanamuphe chifukwa anadzichepetsa komanso analapa mochokera pansi pa mtima.

Davide ankafuna kumanga kachisi wa Yehova. Koma Yehova anasankha mwana wake Solomo kuti ndi amene adzamange kachisiyo. Davide anayamba kusonkhanitsa zinthu zoti Solomo adzagwiritse ntchito pomanga. Iye anati: ‘Kachisi wa Yehova akufunika adzakhale wokongola  kwambiri. Popeza Solomo adakali mwana, ndimuthandiza kupeza zipangizo zomangira kachisiyu.’ Choncho Davide anapereka ndalama zambiri zoti zidzathandize pa ntchito yomanga kachisi. Anapeza anthu aluso komanso anasonkhanitsa golide ndi siliva wambiri. Ndiponso anasonkhanitsa matabwa a mtengo wa mkungudza ochokera ku Turo ndi ku Sidoni. Davide atatsala pang’ono kumwalira, anapatsa Solomo pulani ya kachisi. Anati: ‘Yehova anandiuza kuti ndikulembere pulaniyi. Usachite mantha chifukwa iye akuthandiza. Limba mtima ndipo yamba kugwira ntchitoyi.’

“Wobisa machimo ake zinthu sizidzamuyendera bwino, koma woulula n’kuwasiya adzachitiridwa chifundo.”​—Miyambo 28:13