Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo

 MUTU 40

Davide Anapha Goliyati

Davide Anapha Goliyati

Yehova anauza Samueli kuti: ‘Pita kunyumba ya Jese. Mwana wake wina adzakhala mfumu ya Isiraeli.’ Samueli anapitadi ndipo ataona mwana woyamba wa Jese anaganiza kuti: ‘Amene adzakhale mfumu uja ndi ameneyu.’ Koma Yehova anauza Samueli kuti si ameneyo. Kenako anamuuzanso kuti: ‘Ine ndimaona mtima wa munthu osati zimene anthu amaona.’

Jese anabweretsa ana ake ena 6 koma Samueli anati: ‘Apa palibe aliyense amene Yehova wamusankha. Kodi uli ndi mwana wina?’ Jese anati: ‘Watsala mmodzi wamng’ono kwambiri. Dzina lake Davide. Akudyetsa nkhosa uko.’ Davide atafika, Yehova anauza Samueli kuti: ‘Ndasankha ameneyo.’ Samueli anathira mafuta pamutu pa Davide. Izi zinatanthauza kuti wamudzoza kuti adzakhale mfumu ya Isiraeli.

Pa nthawi ina, Aisiraeli ankamenyana ndi Afilisiti. Ndiyeno kumbali ya Afilisitiwo kunali chimunthu chachikulu komanso champhamvu dzina lake Goliyati. Tsiku lililonse, Goliyati ankanyoza Aisiraeli. Ankanena kuti: ‘Tumizani munthu woti amenyane ndi ineyo. Akapambana, ife tikhala akapolo anu. Koma ine ndikapambana, mukhala akapolo athu.’

Davide anafika pamalo pamene panali asilikali a Isiraeli n’cholinga choti apereke chakudya kwa abale ake. Ali komweko, anamva zimene Goliyati ankanena. Davide anati: ‘Ine ndikamenyana naye ameneyu.’ Mfumu Sauli atamva anati: ‘Iwe wachepa nazo.’ Davide anayankha kuti: ‘Yehova andithandiza.’

 Sauli anauza Davide kuti atenge zida ndi zovala zake koma iye anati: ‘Sindingathe kumenya nkhondo ndi zinthu zonsezi.’ Choncho anangotenga chinthu choponyera miyala chotchedwa gulaye n’kutsetserekera kukamtsinje. Ndiyeno anatola miyala yosalala bwino 5 n’kuika m’kachikwama kake. Kenako anayamba kuthamangira kumene kunali Goliyati. Goliyatiyo atamuona anati: ‘Mwana iwe! Bwera ndikuphe ndipo ukhala chakudya cha mbalame ndi nyama.’ Davide sanachite mantha. M’malomwake anamuyankha kuti: ‘Iwe ukubwera ndi lupanga komanso mkondo koma ine ndikubwera m’dzina la Yehova. Sukumenyana ndi ife ayi koma ndi Mulungu. Lero aliyense adziwa kuti Yehova ndi wamphamvu kuposa lupanga ndi mkondo. Iye atithandiza kuti tikugonjetseni nonsenu.’

Kenako Davide anaika mwala pagulaye uja n’kuuponya mwamphamvu kwambiri. Yehova anamuthandiza moti mwalawo unathamanga n’kukaboola mutu wa Goliyati pachipumi. Nthawi yomweyo Goliyati anagwa n’kufa. Afilisiti ataona zimenezi anayamba kuthawa. Kodi iweyo umadalira Yehova ngati mmene Davide ankachitira?

“Kwa anthu n’zosathekadi, koma sizili choncho kwa Mulungu, pakuti zinthu zonse n’zotheka ndi Mulungu.”​—Maliko 10:27

Onaninso

PHUNZITSANI ANA ANU

Davide Sankachita Mantha

Werengani nkhaniyi m’Baibulo kuti mudziwe zimene zinamuthandiza Davide kuti akhale wolimba mtima.

ZITHUNZI ZOFOTOKOZA NKHANI ZA M’BAIBULO

Davide Anachita Zinthu Molimba Mtima

N’chiyani chinamuchititsa Davide kukhulupirira kuti akhoza kugonjetsa Goliyati? N’chifukwa chiyani inunso muyenera kulimba mtima kuti muchite zinthu zabwino?

ZOTI ANA ACHITE POPHUNZIRA

Imbani Nyimbo Yothandiza Kukhala Olimba Mtima

Phunzirani nyimbo imene imatithandiza kukhala olimba mtima ndipo kenako muimbe limodzi ndi banja lanu.

ZITHUNZI

Davide Anabwera M’dzina la Mulungu

Thandizani ana anu kuti adziwe zimene dzina la Mulungu limatanthauza.

ZITHUNZI

Davide Analimba Mtima Ngakhale Kuti Anali ndi Zida Zochepa

Fananitsani anthu otchulidwa m’Baibulo ndi zinthu zokhudza anthuwo.