Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo

Mawu Ofotokoza Chigawo 7

Mawu Ofotokoza Chigawo 7

Chigawochi chikufotokoza mbiri ya moyo wa Mfumu Sauli komanso Mfumu Davide. Mbiriyi inachitika pafupifupi kwa zaka 80. Poyamba Sauli anali wodzichepetsa komanso ankamvera Mulungu. Koma kenako anasintha n’kusiya kutsatira malangizo a Yehova. Zitatero Yehova anamukana ndipo patapita nthawi anauza Samueli kuti adzoze Davide kuti akhale mfumu. Sauli ankachitira nsanje Davide ndipo mobwerezabwereza anayesa kuti amuphe koma Davideyo sanabwezere. Mwana wa Sauli dzina lake Yonatani, ankadziwa kuti Davide wasankhidwa ndi Yehova choncho anakhala wokhulupirika kwa Davideyo. Davide anachita machimo ena akuluakulu koma nthawi zonse  ankamvera Yehova akamudzudzula. Ngati ndinu kholo, thandizani mwana wanu kuti aziona kufunika kotsatira malangizo a Mulungu nthawi zonse.