Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo

 MUTU 29

Yehova Anasankha Yoswa

Yehova Anasankha Yoswa

Mose anatsogolera mtundu wa Aisiraeli kwa zaka zambiri. Ndiyeno atatsala pang’ono kumwalira, Yehova anamuuza kuti: ‘Iweyo sudzalowetsa Aisiraeli m’Dziko Lolonjezedwa. Koma ndidzangokuonetsa dzikolo.’ Zitatero Mose anapempha Yehova kuti asankhe mtsogoleri wina woti azitsogolera anthuwo. Yehova anamuuza kuti: ‘Pita kwa Yoswa ndipo ukamuuze kuti ndi amene ndamusankha.’

Mose anauza Aisiraeli kuti popeza iye anali atatsala pang’ono kumwalira, Yehova anasankha Yoswa kuti awatsogolere polowa m’Dziko Lolonjezedwa. Ndiyeno Mose anauza Yoswa kuti: ‘Usachite mantha, Yehova akuthandiza.’ Atatero, Mose anapita pamwamba paphiri la Nebo. Kumeneko Yehova anamuonetsa dziko limene analonjeza Abulahamu, Isaki ndi Yakobo. Kenako Mose anamwalira ndipo n’kuti ali ndi zaka 120.

Ndiyeno Yehova anauza Yoswa kuti: ‘Muwoloke mtsinje wa Yorodano ndi kulowa m’dziko la Kanani. Ndizikuthandiza ngati mmene ndinkachitira ndi Mose. Uziwerenga malamulo anga tsiku lililonse. Khala wolimba mtima ndipo usachite mantha. Pita ukachite zimene ndakuuza.’

 Yoswa anatumiza anthu awiri kuti akaone mzinda wa Yeriko. M’nkhani yotsatira tidzaona zimene zinachitika anthuwo atafika kumeneko. Atabwerako iwo ananena kuti tsopano inali nthawi yoti Aisiraeliwo alowe m’dziko la Kanani. Tsiku lotsatira, Yoswa anauza Aisiraeli kuti anyamuke. Kenako anauza ansembe omwe ananyamula likasa la pangano kuti atsogole kupita kumtsinje wa Yorodano. Pa nthawiyi n’kuti madzi a mumtsinjewu atasefukira. Koma ansembewo atangoponda m’madzimo, mtsinjewo unayamba kuuma. Iwo anayenda n’kufika pakati pamtsinjewo ndipo anaima pomwepo mpaka Aisiraeli onse anawoloka. Mwina zimene zinachitikazi zinawakumbutsa zomwe Yehova anachita pa Nyanja Yofiira.

Atayenda kwa zaka zambiri, tsopano Aisiraeli anafika m’Dziko Lolonjezedwa. Iwo anayamba kumanga nyumba ndi mizinda. Analima minda n’kudzala mphesa, zipatso ndi mbewu zosiyanasiyana. Linalidi dziko loyenda mkaka ndi uchi.

“Yehova azidzakutsogolerani nthawi zonse ndipo adzakukhutiritsani ngakhale m’dziko louma.”​—Yesaya 58:11

Onaninso

MAKADI A ANTHU OTCHULIDWA M’BAIBULO

Khadi la m’Baibulo Lonena za Yoswa

Kodi Yoswa ndi asilikali ake anagwetsa bwanji mpanda wa Yeriko? Sindikizani khadi la m’Baibuloli kuti mudziwe zambiri za munthu wolimba mtima wotchulidwa m’Baibuloyu.