Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo

 MUTU 30

Rahabi Anabisa Aisiraeli Okaona Dziko

Rahabi Anabisa Aisiraeli Okaona Dziko

Aisiraeli awiri amene anatumidwa kukaona mzinda wa Yeriko anakafikira m’nyumba ya mayi wina dzina lake Rahabi. Mfumu ya kumeneko itazindikira, inatumiza asilikali kunyumbayo. Koma Rahabi anabisa Aisiraeliwo padenga n’kuuza asilikaliwo kuti alowere njira ina. Kenako anauza Aisiraeliwo kuti: ‘Ndikukuthandizani chifukwa ndikudziwa kuti Yehova akukumenyerani nkhondo ndipo mugonjetsa mzindawu. Chonde, lonjezani kuti simudzandipha ineyo ndi abale anga.’

Aisiraeliwo anauza Rahabi kuti: ‘Tikulonjeza kuti aliyense amene adzakhale m’nyumba yakoyi sadzaphedwa.’ Ndiyeno anamulangiza kuti: ‘Umangirire chingwe chofiira pawindo kuti iwe ndi abale ako mudzatetezeke.’

Rahabi anagwiritsa ntchito chingwe potulutsira Aisiraeli awiriwo pawindo kuti azipita. Iwo anakabisala m’mapiri kwa masiku atatu asanabwerere kumene kunali Yoswa. Kenako Aisiraeli anawoloka mtsinje wa Yorodano kuti ayambe kulanda dzikolo. Mzinda woyamba kuugonjetsa unali wa Yeriko. Yehova anawauza kuti azizungulira mzindawo kamodzi patsiku kwa  masiku 6. Koma pa tsiku la 7 anawauza kuti auzungulire maulendo 7. Kenako ansembe ankaimba malipenga ndipo asilikali ankachita phokoso kwambiri. Zitatero, makoma a mzindawo anagwa. Koma nyumba ya Rahabi yomwe inalumikizana ndi khomalo, sinagwe. Rahabi ndi anthu a m’banja lake anapulumuka chifukwa chakuti ankakhulupirira kwambiri Yehova.

‘Kodi Rahabi sanaonedwe ngati wolungama chifukwa cha ntchito zake, powalandira bwino azondi aja ndi kuwabweza kwawo powasonyeza njira ina?’​—Yakobo 2:25

Onaninso

ZITHUNZI ZOFOTOKOZA NKHANI ZA M’BAIBULO

Rahabi Anatsatira Malangizo

Banja limodzi linapulumuka nthawi imene mzinda wa Yeriko unagwa.

PHUNZITSANI ANA ANU

Rahabi Ankakhulupirira Yehova

Werengani nkhaniyi kuti mmene Rahabi ndi abale ake anapulumukira pamene mzinda wa Yeriko unkawonongedwa.