Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo

 MUTU 37

Yehova Analankhula ndi Samueli

Yehova Analankhula ndi Samueli

Eli anali Mkulu wa Ansembe ndipo anali ndi ana awiri amene ankatumikira ngati ansembe kuchihema. Mayina awo anali Hofeni ndi Pinehasi. Anawa sankamvera malamulo a Yehova ndipo ankachitira anthu zoipa. Aisiraeli akabweretsa nsembe zoti apereke kwa Yehova iwo ankatengapo nyama yabwino n’kukadya. Eli anamva zimene ana akewa ankachita koma sanawathandize. Kodi Yehova anangoilekerera nkhaniyi?

Pa nthawiyo Samueli anali wamng’ono koma sanatengere makhalidwe oipawo ndipo Yehova ankasangalala naye. Tsiku lina atagona anamva munthu akumuitana. Iye anadzuka n’kupita kwa Eli ndipo atafika anati: ‘Ndabwera.’ Koma Eli anati: ‘Inetu sindinakuitane. Pita ukagone.’ Samueli atabwerera anamvanso kuitana kachiwiri. Ulendo wachitatu, Eli anazindikira kuti amene akumuitana ndi Yehova. Ndiyeno anamuuza kuti, akakamuitananso akayankhe kuti: ‘Lankhulani Yehova. Ine mtumiki wanu ndikumva.’

Samueli atapita kukagona anamvanso kuitana kuti: ‘Samueli! Samueli!’ Iye anayankha kuti: ‘Lankhulani. Ine mtumiki wanu ndikumva.’ Ndiyeno Yehova anamuuza kuti: ‘Ukamuuze Eli kuti ndimulanga iyeyo ndi banja lake. Akudziwa zoipa zimene ana ake akuchita kuchihema koma  akungowalekerera.’ Kutacha, Samueli anakatsegula zitseko za chihema ngati mmene ankachitira nthawi zonse. Iye ankaopa kuuza mkulu wa ansembe zimene Yehova ananena. Koma Eli anamuitana n’kumufunsa kuti: ‘Mwana wanga, kodi Yehova anakuuza kuti chiyani? Ndiuze chilichonse.’ Zitatero, Samueli anauza Eli zonse zimene Yehova ananena.

Yehova anapitirizabe kutsogolera Samueli. Anthu a m’dziko lonse la Isiraeli ankadziwa kuti Yehova anasankha Samueli kuti akhale mneneri komanso woweruza.

“Kumbukira Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako.”​—Mlaliki 12:1

Onaninso

ZITHUNZI

Samueli Ali ku Kachisi

Kodi Yehova anadalitsa bwanji Samueli? Koperani chithunzichi, lumikizani timadontho kenako werengani nkhani ya m’Baibulo.

PHUNZITSANI ANA ANU

Samueli Anapitiriza Kuchita Zinthu Zabwino

Kodi mungatsanzire bwanji chitsanzo cha Samueli?

MAKADI A ANTHU OTCHULIDWA M’BAIBULO

Khadi la M’Baibulo Lonena za Samueli

Samueli anayamba kutumikira Mulungu ali wamng’ono. Kodi inuyo mungatsanzire bwanji chitsanzo chake?

ZITHUNZI ZOFOTOKOZA NKHANI ZA M’BAIBULO

Samueli Anasankha Kutumikira Yehova

Samueli ankaona anthu amene ankatumikira pachihema akuchita zinthu zoipa kwambiri. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kupitirizabe kutumikira Yehova pamene anthu ena ankachita zoipa?

TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO

Samueli “Anapitiriza Kukula, Akukondedwa Ndi Yehova”

N’chifukwa chiyani tinganene kuti Samueli analeredwa mwapadera? N’chiyani chinkalimbikitsa chikhulupiriro chake pamene anali kuchihema?

ZITHUNZI

Kodi Ndi Ndani Amene Anasankha Kutumikira Yehova?

Zochitazi zimathandiza ana a pakati pa zaka 6 ndi 8 kuti adziwe anthu otchulidwa m’Baibulo.