Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 23

Analonjeza Kuti Azimvera Yehova

Analonjeza Kuti Azimvera Yehova

Patadutsa miyezi iwiri chichokereni ku Iguputo, Aisiraeli anafika paphiri la Sinai ndipo anamanga misasa. Yehova anauza Mose kuti akwere m’phirimo. Kumeneko anamuuza kuti: ‘Ndapulumutsa Aisiraeli. Ngati angandimvere komanso kusunga malamulo anga, adzakhala anthu anga apadera.’ Mose anatsika m’phirimo n’kukauza Aisiraeli zimene Yehova ananenazi. Kodi iwo anatani atamva zimenezi? Anayankha kuti: ‘Tidzachita chilichonse chimene Yehova wanena.’

Mose anapitanso kuphiri kuja. Ndiyeno Yehova anamuuza kuti: ‘Ndilankhula nanu pakadutsa masiku atatu. Uchenjeze anthu kuti asakwere phirili.’ Mose anatsika n’kukauza Aisiraeli kuti akonzekere kumva zimene Yehova adzawauze.

Patadutsa masiku atatu, kunayamba kuchita mphenzi ndi mabingu ndipo paphiri lonselo panali mtambo wakuda. Kunamvekanso kulira kwa mphamvu kwa lipenga. Ndiyeno paphiripo panali moto kusonyeza kuti Yehova watsikirapo. Aisiraeli anachita mantha kwambiri moti anayamba kunjenjemera. Phiri lonselo linkafuka utsi komanso linkagwedezeka kwambiri. Nalonso phokoso la lipenga lija linkawonjezekawonjezeka. Ndiyeno Mulungu anati: ‘Ine ndine Yehova. Musamalambire milungu ina.’

Mose anakweranso m’phiri muja ndipo Yehova anamupatsa malamulo oti anthuwo azitsatira pomulambira komanso pochita zinthu zatsiku ndi tsiku. Mose analemba malamulowo n’kukawawerengera Aisiraeli. Iwo analonjeza kuti: ‘Tidzachita zonse zimene Yehova wanena.’ Aisiraeliwo analonjeza kuti azimvera Mulungu. Koma kodi anachitadi zimenezi?

“Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.”​—Mateyu 22:37