Patangotha miyezi iwiri kuchokera pamene anawoloka Nyanja Yofiira, Aisiraeli anafika paphiri la Sinai. Paphirili, Yehova anachita nawo pangano loti akhale anthu ake apadera. Iye ankawateteza komanso kuwapatsa zofunika pa moyo. Ankawapatsa malo abwino oti azikhala, chakudya chothedwa mana komanso zovala zawo sizinkatha. Ngati ndinu kholo, thandizani mwana wanu kudziwa chifukwa chake Yehova anapatsa Aisiraeli Chilamulo, chihema komanso ansembe. Tsindikani ubwino wochita zimene talonjeza, kukhala odzichepetsa komanso okhulupirika kwa Yehova.