Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo

 MUTU 14

Kapolo Amene Ankamvera Mulungu

Kapolo Amene Ankamvera Mulungu

Yosefe anali wachiwiri kwa mwana womaliza wa Yakobo. Azichimwene ake anaona kuti bambo awo ankamukonda kwambiri. Kodi ukuganiza kuti iwo anasangalala ndi zimenezi? Ayi. Ankamuchitira nsanje komanso ankadana naye. Pa nthawi ina Yosefe analota maloto odabwitsa. Atawauza azichimwene akewo, iwo anaganiza kuti malotowo akutanthauza kuti tsiku lina adzamugwadira. Izi zinangowonjezera chidani chija.

Pa nthawi ina azichimwene ake a Yosefe ankadyetsa ziweto pafupi ndi mzinda wotchedwa Sekemu. Ndiyeno Yakobo anatuma Yosefe kuti akawaone ngati ali bwino. Koma iwo atamuona akubwera anayamba kuuzana kuti: ‘Wolota uja suyo akubwera apoyo? Tiyeni timuphe.’ Atatero anamugwira n’kumuponyera m’chitsime chakuya. Koma mmodzi mwa azichimwene akewo dzina lake Yuda, anati: ‘Ayi tisamuphe. Tiyeni tingomugulitsa kuti akhale kapolo.’ Choncho anamugulitsa ndi ndalama zasiliva zokwana 20 kwa amalonda achimidiyani omwe ankapita ku Iguputo.

Kenako azichimwene akewo anatenga mkanjo wa Yosefe n’kuuviika m’magazi a mbuzi. Ndiyeno atafika kunyumba anapatsa bambo awo mkanjowo n’kunena kuti: ‘Kodi mkanjo uwu mungauzindikire? Kapena ndi wa Yosefe?’ Yakobo atauona, anaganiza kuti Yosefe wadyedwa ndi chilombo. Choncho anamva chisoni kwambiri n’kuyamba kulira ndipo sankatonthozeka.

Amalonda aja atafika ku Iguputo, anamugulitsa Yosefe kwa munthu wina waudindo dzina lake Potifara. Choncho Yosefe anali kapolo. Koma Yehova anali naye. Potifara anaona kuti Yosefe anali wolimbikira ntchito komanso wodalirika. Pasanapite nthawi anaikidwa kuti aziyang’anira zinthu zonse za Potifara.

 Mkazi wa Potifara anaona kuti Yosefe anali wooneka bwino komanso wamphamvu. Tsiku lililonse ankamuuza kuti agone naye. Koma Yosefe ankakana ndipo anamuuza kuti: ‘Ayi, zimenezo si zabwino. Abwana anga amandikhulupirira ndipo inuyo ndinu mkazi wawo. Ndikagona nanu ndichimwira Mulungu.’

Tsiku lina mkazi wa Potifara anakakamizanso Yosefe kuti agone naye. Moti anamugwira malaya koma Yosefe anathawa. Potifara atabwera, mkaziyo ananama kuti Yosefe amafuna kumugwiririra. Choncho Potifara anakwiya kwambiri ndipo anaika Yosefe m’ndende. Koma Yehova sanamuiwale.

“Dzichepetseni pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu, kuti adzakukwezeni m’nthawi yake.”​—1 Petulo 5:6

Onaninso

ZITHUNZI ZOFOTOKOZA NKHANI ZA M’BAIBULO

Yosefe Ali ku Iguputo

Kodi mungasangalatse bwanji Mulungu ngakhale pamene anthu ena sakuona? Werengani nkhani ya m’Baibuloyi kuti muone chitsanzo cha Yosefe.

ZOTI MUCHITE POPHUNZIRA BAIBULO

Yosefe, Anaimbidwa Mlandu Womunamizira

Yosefe anaikidwa m’ndende pa mlandu womunamizira. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kupirira?

ZITHUNZI ZOFOTOKOZA NKHANI ZA M’BAIBULO

Nkhani ya Ana a Yakobo

Kodi muyenera kutani ngati m’bale wanu kapena mnzanu wapeza chinthu chimene inuyo mumachifuna kwambiri?

ZITHUNZI

Yosefe Anagulitsidwa N’kukhala Kapolo

Koperani ndi kusindikiza chithunzichi ndipo pezani zinthu ziwiri zimene sizikugwirizana ndi nkhani ya m’Baibuloyi.

MAKADI A ANTHU OTCHULIDWA M’BAIBULO

Khadi la M’Baibulo Lonena za Yosefe

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe chifukwa chake Farao anasankha Yosefe kukhala womutsatira m’dziko la Iguputo

MAKADI A ANTHU OTCHULIDWA M’BAIBULO

Khadi la M’Baibulo Lonena za Potifara

Koperani khadi la munthu wotchulidwa m’Baibuloli kuti mudziwe za Potifara, yemwe anali bwana wa Yosefe ku Iguputo.

ZOTI MUCHITE POPHUNZIRA BAIBULO

Zimene Mungachite Kuti Muzipewa Mayesero

Pamene Yosefe ankayesedwa kuti achite chigololo, kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti achite zinthu zoyenera?