Kudziko lina lotchedwa Uzi kunali munthu wina amene ankalambira Yehova. Dzina lake anali Yobu. Iye anali ndi banja lalikulu ndipo anali wolemera kwambiri. Yobu anali wokoma mtima ndipo ankathandiza anthu osauka, azimayi amasiye komanso ana amasiye. Koma kodi iye sankakumana ndi mavuto chifukwa choti anali munthu wabwino? Ayi.

Satana ankaona zonse zimene Yobu ankachita, ngakhale kuti Yobuyo sankadziwa zimenezi. Yehova anauza Satana kuti: ‘Kodi waona mtumiki wanga Yobu? Padziko lapansi palibe munthu wolungama ngati iyeyu. Iye amandimvera komanso amachita zoyenera.’ Satana anayankha kuti: ‘N’zoona kuti Yobu amakumverani. Koma n’chifukwa choti mumamuteteza komanso kumudalitsa. Mwamupatsa malo abwino komanso ziweto. Koma mutamulanda zinthu zimenezi akhoza kusiya kukumverani.’ Yehova anati: ‘Ndakulola kuti umuyese, koma usamuphe.’ N’chifukwa chiyani Yehova analola kuti Satana ayese Yobu? N’chifukwa choti ankadziwa kuti Yobu akhalabe wokhulupirika.

Satana anayamba kuyesa Yobu pomubweretsera mavuto osiyanasiyana. Choyamba anachititsa kuti anthu otchedwa Asabeya abe ng’ombe ndi abulu ake. Kenako moto unatentha nkhosa zake. Ndiye panabweranso anthu otchedwa Akasidi amene anadzaba ngamila zake zonse. Komanso antchito amene ankayang’anira ziweto za Yobu anaphedwa. Komatu si zokhazi. Tsiku lina ana onse a Yobu anali m’nyumba ina n’kumachita phwando. Koma mwadzidzidzi nyumbayo inagwa n’kupha onsewo. Yobu anamva chisoni kwambiri ndi zonsezi komabe sanasiye kulambira Yehova.

Satana anaganiza kuti Yobu akhoza kusiya kumvera Mulungu atakumana ndi mavuto enanso. Choncho  anachititsa kuti Yobu atuluke zilonda zowawa kwambiri thupi lonse. Yobu sankadziwa chimene chinkachititsa zonsezi koma anapitiriza kumvera Yehova. Mulungu ankaona zonsezi ndipo anasangalala kwambiri kuona kuti Yobu anakhalabe wokhulupirika.

Kenako Satana anatumiza azibambo atatu kwa Yobu. Iwo anauza Yobu kuti: ‘Uyenera kuti unachimwira Mulungu ndipo unabisa. Ndiye Mulungu akukulanga chifukwa cha zimenezo.’ Yobu anati: ‘Palibe chilichonse cholakwika chimene ndinachita.’ Koma zitatere Yobu anayamba kuganiza kuti Yehova ndi amene akuchititsa mavuto ake ndipo sakuchita chilungamo.

Munthu wina wamng’ono kuposa azibambo atatu aja, dzina lake Elihu, ankangomvetsera pamene anthuwa ankakambirana. Koma kenako anayankha kuti: ‘Zimene nonsenu mukunena si zoona. Yehova ndi wapamwamba kwambiri ndipo anthufe sitingathe kumvetsa zochita zake zonse. Iye sangachite zinthu zoipa. Amaona zonse ndipo anthu akamavutika amawathandiza.’

Ndiyeno Yehova analankhula ndi Yobu kuti: ‘Kodi unali kuti pamene ndinkalenga kumwamba ndi dziko lapansi? N’chifukwa chiyani ukunena kuti ndikupanga zinthu zopanda chilungamo? Ukungolankhulatu zinthu zimene sukuzidziwa.’ Yobu anazindikira kuti ankaganiza molakwika ndipo anati: ‘Pepani ndalakwa. Ndinkangomva za inu, koma panopa ndakudziwani. Palibe chimene simungathe kuchita. Mundikhululukire chifukwa cha zomwe ndinanena.’

Kenako mayesero a Yobu anatha ndipo Yehova anamuchiritsa. Anamupatsanso zinthu zambiri kuposa zomwe anali nazo poyamba. Yobu anakhala ndi moyo wosangalala komanso wautali. Yehova anamudalitsa chifukwa choti ankamumvera ngakhale pa mavuto. Kodi iwenso ungakhale ngati Yobu n’kumamvera Yehova zivute zitani?

“Munamva za kupirira kwa Yobu ndipo mwaona zimene Yehova anamupatsa, mwaona kuti Yehova ndi wachikondi chachikulu ndi wachifundo.”—Yakobo 5:11