Mose anauza Farao kuti sadzapitanso kukaonana naye. Koma asananyamuke, anamuuza kuti: ‘Lero pakati pa usiku ana onse aamuna oyamba kubadwa a Aiguputo afa, kuyambira mwana wa Farao mpaka ana a akapolo.’

Yehova anauza Aisiraeli kuti adye chakudya chapadera. Anawauza kuti: ‘Mupeze mwana wankhosa kapena wambuzi. Akhale wamphongo komanso wachaka chimodzi. Mumuphe ndipo magazi ake mupake pamafelemu a zitseko zanu. Nyama yakeyo muiwotche ndipo muidye limodzi ndi mikate yopanda chofufumitsa. Mudye mutavala zovala zanu komanso nsapato pokonzekera ulendo. Usiku wa lero mutuluka mu Iguputo.’ Kodi ukuganiza kuti Aisiraeli anamva bwanji atauzidwa zimenezi?

Pakati pa usiku, mngelo wa Yehova anapita kunyumba zonse za mu Iguputo. Nyumba iliyonse imene inalibe magazi pafelemu, mwana woyamba anafa. Koma mngeloyo sankapha ana a m’nyumba zimene anapaka magazi pamafelemu. M’banja lililonse la Aiguputo, kaya lolemera kapena losauka, munafa mwana woyamba. Koma palibe mwana ngakhale mmodzi wa Aisiraeli amene anafa.

Mwana woyamba wa Farao weniweniyo anafanso. Apa m’pamene makani a Farao anathera. Nthawi yomweyo anauza Mose ndi Aroni kuti: ‘Nyamukani. Chokani kuno. Pitani mukalambire Mulungu wanu. Mutengenso ziweto zanu.’

 Usiku womwewo, Aisiraeli ananyamuka ndipo kunja kunali kukuwala kwambiri chifukwa mwezi unali wathunthu. Mabanja komanso mafuko ankayendera limodzi. Panali amuna 600,000 komanso akazi ndi ana ambiri. Panalinso anthu a mitundu ina amene anapita nawo kuti akalambirenso Yehova. Apa m’pamene panathera ukapolo wa Aisiraeli.

Pofuna kukumbukira zimene Yehova anachita powapulumutsa, Aisiraeliwa ankadya chakudya chapadera chija chaka chilichonse. Mwambowu ankautchula kuti Pasika.

“Ndakusiya ndi moyo kuti ndikusonyeze mphamvu zanga, ndi kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.”​—Aroma 9:17