Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo

 MUTU 15

Yehova Sanamuiwale Yosefe

Yehova Sanamuiwale Yosefe

Yosefe ali m’ndende, Farao yemwe anali mfumu ya ku Iguputo, analota maloto. Palibe amene ankadziwa tanthauzo la malotowo. Wantchito wina wa Farao ananena kuti Yosefe akhoza kufotokoza tanthauzo lake. Nthawi yomweyo, Farao anaitanitsa Yosefe.

Atafika, Farao anamufunsa kuti: ‘Kodi ungandiuze tanthauzo la maloto anga?’ Yosefe anayankha kuti: ‘Pa zaka 7 zikubwerazi, mu Iguputo muno mukhala zakudya zambirimbiri koma kenako kudzabwera zaka zina 7 za njala. Musankhe munthu wanzeru kuti asonkhanitse chakudya kuti anthu anu asadzafe ndi njala.’ Farao anayankha kuti: ‘Ndakusankha iweyo. Ukhala wachiwiri wanga.’ Kodi Yosefe anadziwa bwanji tanthauzo la maloto a Farao? Yehova ndi amene anamuthandiza.

Ndiyeno Yosefe anasonkhanitsa chakudya kwa zaka 7. Kenako padziko lonse panali njala ngati mmene iye ananenera. Anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana ankabwera kudzagula chakudya kwa Yosefe. Ndiyeno bambo ake atamva kuti ku Iguputo kuli chakudya, anatuma ana awo 10 kuti apite kukagula chakudya.

Ana a Yakobo anapita kwa Yosefe ndipo iye atangowaona anawazindikira. Koma azichimwene akewo sanamuzindikire. Iwo anamugwadira ndipo izi zinali zogwirizana ndi maloto amene Yosefe analota ali wamng’ono. Koma iye ankafuna kudziwa ngati abale akewo adakali ndi chidani. Choncho anawauza kuti: ‘Inu ndinu akazitape! Mwabwera kuno kudzafufuza malo amene dziko lathu lili lofooka.’ Iwo anayankha kuti: ‘Ayi ndithu. Tachokera ku Kanani ndipo m’banja lathu tinalimo amuna 12. M’bale wathu wina anamwalira ndipo wamng’ono watsala ndi bambo athu.’ Kenako Yosefe  anati: ‘Mukabwere ndi mng’ono wanuyo kuti ndikukhulupirireni.’ Zitatero azichimwene ake a Yosefewo anabwerera kwawo.

Ndiyeno chakudya chija chitatha, Yakobo anauza ana akewo kuti apitenso ku Iguputo. Pa ulendowu anatenga mng’ono wawo uja ndipo dzina lake linali Benjamini. Pofuna kuwayesa abale akewo, Yosefe anabisa kapu yake m’thumba la Benjamini n’kuwauza kuti aba kapuyo. Antchito a Yosefe anapeza kapuyo m’thumba la Benjamini ndipo izi zinadabwitsa kwambiri abale akewo. Iwo anapempha Yosefe kuti awalange iwowo m’malo mwa Benjamini.

Apa Yosefe anadziwa kuti abale akewo asintha kwambiri. Iye analephera kudzigwira moti anayamba kulira n’kunena kuti: ‘Ndine Yosefe, m’bale wanu uja. Kodi bambo adakali moyo?’ Abale akewo anadabwa kwambiri. Koma iye anawauza kuti: ‘Musadandaule ndi zimene munandichitira zija. Mulungu ndi amene ananditumiza kuno kuti akupulumutseni. Pitani mukatenge bambo mubwere nawo kuno.’

Abale akewo anapita kukauza bambo awo nkhani yabwinoyi ndipo anawatenga n’kupita nawo ku Iguputo. Yosefe ndi bambo akewo atakumananso anasangalala kwambiri chifukwa panali patadutsa zaka zambiri asanaonane.

“Ngati simukhululukira anthu machimo awo, Atate wanu sadzakukhululukirani machimo anu.”—Mateyu 6:15

Onaninso

ZITHUNZI ZOFOTOKOZA NKHANI ZA M’BAIBULO

Yosefe Anapulumutsa Anthu Ambiri

Koperani nkhaniyi kuti muwerenge zokhudza Yosefe, amene Mulungu anamugwiritsira ntchito kupulumutsa mtundu wonse.

ZITHUNZI ZOFOTOKOZA NKHANI ZA M’BAIBULO

Yosefe Ali ku Iguputo

Kodi mungasangalatse bwanji Mulungu ngakhale pamene anthu ena sakuona? Werengani nkhani ya m’Baibuloyi kuti muone chitsanzo cha Yosefe.

MAKADI A ANTHU OTCHULIDWA M’BAIBULO

Khadi la M’Baibulo Lonena za Yosefe

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe chifukwa chake Farao anasankha Yosefe kukhala womutsatira m’dziko la Iguputo

ZITHUNZI

Farao Anapatsa Yosefe Udindo Waukulu

Malizitsani kujambula chithunzichi kuti mudziwe chifukwa chake abale ake a Yosefe analephera kumuzindikira.

ZOTI ANA ACHITE POPHUNZIRA

Anthu Otchulidwa M’Baibulo Amene Akufanana ndi Yosefe

Koperani ndi kusindikiza nkhaniyi ndiyeno lembani kufanana pakati pa Yosefe ndi anthu ena asanu otchulidwa m’Baibulo.

ZOTI ANA ACHITE POPHUNZIRA

Mafunso: Analankhula Izi Ndani? (Genesis 41-50)

Koperani nkhaniyi ndipo muyese kulumikiza mawuwo ndi munthu amene anawalankhula.