Chigawochi chikufotokoza nkhani ya Yosefe, Yobu, Mose komanso Aisiraeli. Onsewa anapirira mayesero osiyanasiyana ochokera kwa Mdyerekezi. Ena mwa anthuwa anachitiridwa zinthu zopanda chilungamo, kuikidwa m’ndende ngakhalenso kuphedwa kumene. Koma Yehova anawateteza m’njira zosiyanasiyana. Ngati ndinu kholo, thandizani mwana wanu kumvetsa mmene atumiki a Yehova amenewa anavutikira koma n’kukhalabe okhulupirika.

Yehova anagwiritsa ntchito Miliri 10 pofuna kusonyeza kuti iyeyo ndi wamphamvu kwambiri kuposa milungu ya Aiguputo. Fotokozani mmene Yehova anatetezera anthu ake m’mbuyomu komanso mmene akuwatetezera masiku ano.