Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo

 MUTU 10

Kumbukirani Mkazi wa Loti

Kumbukirani Mkazi wa Loti

Loti ankakhala ndi Abulahamu ku Kanani. Kenako onse anakhala ndi ziweto zambiri moti malo odyetsera ziwetozo anawachepera. Ndiyeno Abulahamu anauza Loti kuti: ‘N’zosatheka kuti tizikhalabe limodzi. Yamba iweyo kusankha kumene ukufuna kukhala ndipo ine ndipita kwinako.’ Apatu Abulahamu anasonyeza kuti sanali wodzikonda.

Loti anasankha dera lapafupi ndi mzinda wa Sodomu. Iye anakopeka ndi derali chifukwa linali ndi madzi ambiri komanso udzu wobiriwira. Choncho anasamukira kumeneku ndi banja lake.

Anthu a mumzinda wa Sodomu komanso mzinda wina wapafupi wotchedwa Gomora anali ndi makhalidwe oipa kwambiri. Choncho Mulungu anaona kuti ndi bwino kungowononga mizindayo. Koma anaganiza zoti apulumutse Loti ndi banja lake. Iye anatumiza angelo awiri kukawauza kuti: ‘Nyamukani msanga. Chokani mumzindawu chifukwa Yehova akufuna kuuwononga.’

Koma Loti ndi banja lake ankangochedwachedwa moti angelowo anachita kuwagwira manja n’kuwatulutsa mumzindawo. Iwo anawauza kuti: ‘Fulumirani mungafe. Komanso musayang’ane m’mbuyo. Mukangoyang’ana mufa.’

Iwo atafika mumzinda wa Zoari, Yehova anavumbitsa moto ndi sulufule mumzinda wa Sodomu ndi Gomora. Mizinda yonseyi inapseratu. Koma mkazi wa Loti sanamvere chenjezo lija ndipo anayang’ana m’mbuyo. Atangotero anasanduka chipilala chamchere. Komabe Loti ndi ana ake  aakazi anapulumuka chifukwa choti anamvera Yehova. Onse ayenera kuti anamva chisoni ataona kuti mayi afa chifukwa chosamvera. Koma anasangalalabe kuti iwowo anamvera malangizo a Yehova.

“Kumbukirani mkazi wa Loti.”​—Luka 17:32

Onaninso

ZITHUNZI

Mkazi wa Loti Anasanduka Chipilala Chamchere

Werengani nkhani ya m’Baibulo kenako lumikizani madontho. Kodi mukuphunzira chiyani kwa mkazi wa Loti?

ZITHUNZI ZOFOTOKOZA NKHANI ZA M’BAIBULO

Loti ndi Banja Lake—Zithunzi Zofotokoza Nkhani

Koperani nkhaniyi kuti mudziwe zimene mungaphunzire pa nkhani yokhudza banja la Loti.

MAKADI A ANTHU OTCHULIDWA M’BAIBULO

Khadi la M’Baibulo Lonena za Loti

Koperani khadi la m’Baibuloli kuti mudziwe zambiri za Loti amene anali mwana wa mchimwene wa Abulahamu.