Abulahamu anaphunzitsa mwana wake Isaki kuti azikonda Yehova komanso kukhulupirira malonjezo ake. Koma Isaki ali ndi zaka pafupifupi 25, Yehova anapempha Abulahamu kuti achite zinthu zovuta kwambiri. Kodi anamuuza kuti atani?

Mulungu anauza Abulahamu kuti: ‘Tenga mwana wako mmodzi yekhayo ndipo ukamupereke nsembe kuphiri la Moriya.’ Abulahamu sankadziwa chifukwa chake Mulungu anamuuza kuti achite zimenezi. Komabe iye anamvera.

M’mawa wa tsiku lotsatira, anatenga Isaki komanso antchito ake awiri n’kuyamba ulendo wopita kuphiri la Moriya. Atayenda kwa masiku atatu, anayamba kuona phirilo chapatali. Abulahamu anauza antchito ake aja kuti adikire penapake, pamene iye ndi Isaki akukapereka nsembe. Abulahamu anapatsa Isaki nkhuni kuti anyamule ndipo iye anatenga mpeni. Koma Isaki anafunsa bambo akewo kuti: ‘Nanga nkhosa yokapereka nsembeyo ili kuti?’ Abulahamu anayankha kuti: ‘Mwana wanga, Yehova akatipatsa.’

Atafika paphiripo, anamanga malo operekera nsembe. Ndiyeno Abulahamu anam’manga Isaki manja ndi miyendo n’kumugoneka paguwapo.

Kenako anatenga mpeni kuti amuphe. Koma nthawi yomweyo, anamva mngelo wa Yehova akufuula kuti: ‘Abulahamu, usaphe mnyamatayo. Tsopano ndadziwa kuti umakhulupirira  Mulungu chifukwa umafuna kupereka nsembe mwana wako.’ Zitatero, Abulahamu anaona nkhosa itakodwa m’ziyangoyango, chapafupi. Anamasula nkhosayo n’kuipereka nsembe.

Kuyambira tsiku limenelo, Yehova anayamba kutchula Abulahamu kuti mnzake. Kodi ukudziwa chifukwa chake? Ndi chifukwa choti Abulahamu ankachita zilizonse zimene Yehova ankafuna ngakhale zitakhala kuti sakuzimvetsa.

Yehova anabwerezanso lonjezo limene anamuuza Abulahamu kuti: ‘Ndidzakudalitsa komanso ndidzachulukitsa ana ako.’ Apa Yehova ankatanthauza kuti adzadalitsa anthu onse abwino kudzera m’banja la Abulahamu.

“Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”—Yohane 3:16