Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo

 MUTU 5

Chingalawa cha Nowa

Chingalawa cha Nowa

Patapita nthawi, anthu anachuluka padzikoli, koma ambiri anali oipa. Ngakhalenso angelo ena anali oipa. Iwo anachoka kumwamba n’kubwera padziko lapansi. Kodi ukudziwa chifukwa chake angelowa anachita zimenezi? Ankafuna kuti adzakhale ndi matupi ngati a anthu n’cholinga choti akwatire akazi a padziko lapansi.

Angelowo atakwatira akaziwo, anabereka ana. Anawo anali aatali komanso amphamvu kwambiri ndipo ankavutitsa anthu ena. Yehova sanalole kuti zimenezi zipitirire. Choncho anaganiza zobweretsa chigumula kapena kuti chimvula champhamvu kuti chiwononge anthu oipawo.

Koma panali munthu wina yemwe sankachita zoipa ndipo ankakonda Yehova. Dzina lake anali Nowa. Iye anali ndi mkazi ndi ana aamuna atatu. Mayina awo anali Semu, Hamu ndi Yafeti ndipo onsewa anali ndi akazi. Yehova anauza Nowa kuti apange chingalawa choti iye ndi banja lake apulumukiremo. Chingalawacho chinkaoneka ngati chibokosi chachikulu choti chingathe kuyandama pamadzi. Yehova anauzanso Nowa kuti alowetse nyama zambiri m’chingalawamo kuti nazonso zipulumuke.

Nthawi yomweyo, Nowa anayamba kukhoma chingalawacho. Iye ndi banja lake anagwira ntchitoyi kwa zaka 50. Popanga chingalawacho anatsatira malangizo onse a Yehova. Pa nthawi imeneyi, Nowa ankachenjezanso anthu kuti kubwera Chigumula. Koma palibe amene anamvera.

Kenako, inafika nthawi yoti alowe m’chingalawamo. M’mutu wotsatira tiona zimene zinachitika.

“Monga mmene analili masiku a Nowa, ndi mmenenso kukhalapo kwa Mwana wa munthu kudzakhalire.”​—Mateyu 24:37

Onaninso

MAKADI A ANTHU OTCHULIDWA M’BAIBULO

Khadi la M’Baibulo Lonena za Nowa

Kodi mukudziwa mayina atatu a ana a Nowa? Dziwani zambiri zokhudza Nowa ndi banja lake.

ZITHUNZI ZOFOTOKOZA NKHANI ZA M’BAIBULO

Nowa Ankakhulupirira Kwambiri Mulungu

Nowa anamvera Mulungu ndipo anamanga chingalawa kuti apulumutse banja lake ku chigumula. Kodi nkhani ya Nowa ndi chigumula ikukuphunzitsani chiyani zokhudza kukhulupirira Mulungu?