Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo

 MUTU 6

Anthu 8 Anapulumuka

Anthu 8 Anapulumuka

Nowa ndi banja lake analowa m’chingalawa limodzi ndi nyama. Yehova anatseka chitseko ndipo mvula inayamba kugwa. Inali yambiri moti chingalawa chija chinayamba kuyandama. Kenako madzi anamiza nthaka yonse. Anthu oipa onse amene sanali m’chingalawacho anafa. Koma Nowa ndi banja lake anapulumuka. Iwo ayenera kuti anasangalala kwambiri podziwa kuti anamvera Yehova.

Mvulayo inagwa kwa masiku 40, masana ndi usiku. Kenako inasiya ndipo madzi anayamba kuphwera. Ndiyeno chingalawacho chinaima paphiri. Koma padzikoli panali padakali madzi ambiri choncho Nowa ndi banja lakelo anakhalabe m’chingalawacho.

Madziwo ankaphwera pang’onopang’ono. Nowa ndi banja lakelo anakhala m’chingalawacho nthawi yoposa chaka. Kenako Yehova anawauza kuti atuluke ndipo zinali ngati akulowa m’dziko latsopano. Iwo anathokoza kwambiri Yehova chifukwa chowapulumutsa moti anapereka nsembe.

Yehova anasangalala kwambiri ndi nsembeyo. Iye analonjeza kuti sadzagwiritsanso ntchito chigumula powononga zinthu padzikoli. Potsimikizira zimenezi, anachititsa kuti kumwamba kuoneke utawaleza. Kodi iweyo unauonapo utawaleza?

Kenako Yehova anauza Nowa ndi banja lake kuti akhale ndi ana n’kudzaza dziko lapansi.

“Nowa analowa m’chingalawa. Anthu ananyalanyaza zimene zinali kuchitika mpaka chigumula chinafika n’kuwaseseratu onsewo.”​—Mateyu 24:38, 39