Tsiku lina Hava ali yekha, njoka inabwera n’kuyamba kulankhula naye. Inamufunsa kuti: ‘Eti n’zoona kuti Mulungu anakuletsani kuti musamadye zipatso za mtengo uliwonse m’mundamu?’ Hava anayankha kuti: ‘Ayi. Anangotiletsa zipatso za mtengo umodzi wokha, ndipo anati tikadzadya zipatso zimenezo tidzafa.’ Ndiyeno njokayo inati: ‘Inutu simudzafa. Ndipo mukadya zipatso zimenezi mudzafanana ndi Mulungu.’ Kodi zimenezi zinali zoona? Ayi, linali bodza. Koma Hava anakhulupirira zimene njokayi inanena. Atayamba kuyang’anitsitsa zipatsozo, anayamba kuzisirira. Ndiyeno anathyola chipatso cha mtengowo n’kudya kenako n’kupatsako Adamu. Adamu ankadziwa kuti akapanda kumvera Mulungu adzafa. Koma nayenso anadya.

Madzulo a tsiku lomwelo Yehova analankhula ndi Adamu ndi Hava. Anawafunsa kuti n’chifukwa chiyani sanamvere. Hava anati njoka ndi imene yamuchititsa, ndipo Adamu anati Hava ndi amene wamuchititsa. Chifukwa cha kusamverako, Yehova anawathamangitsa m’munda wa Edeni. Kuti asabwereremonso, Yehova anaika angelo komanso lupanga loyaka moto pamalo olowera m’mundawo.

Yehova ananena kuti njoka nayonso idzalangidwa. Komatu sinali njoka yeniyeni imene inalankhula ndi Hava. Yehova sanalenge njoka zoti zizitha kulankhula. Choncho mngelo woipa ndi amene anachititsa kuti njokayo izilankhula. Anachita izi pofuna kunamiza Hava. Mngelo ameneyo ndi Satana Mdyerekezi. M’tsogolomu, Yehova adzamuwononga kuti asamadzanamizenso anthu.

“Mdyerekezi . . . ndi wopha anthu chiyambire kupanduka kwake, ndipo sanakhazikike m’choonadi, chifukwa mwa iye mulibe choonadi.”​—Yohane 8:44