N’chifukwa chiyani Yehova anabweretsa chigumula chimene chinawononga zamoyo zonse? Kale kwambiri anthu asanachuluke padzikoli, panachitika nkhani inayake. Nkhaniyi inachititsa kuti munthu aliyense azifunika kusankha kuchita zabwino kapena zoipa. Anthu ena monga Adamu, Hava ndi mwana wawo Kaini anasankha kuchita zoipa. Koma panalinso anthu ena ochepa monga Abele ndi Nowa omwe anasankha kuchita zabwino. Pofika nthawi ya Nowa anthu ambiri ankachita zoipa n’chifukwa chake Yehova anawononga dziko loipalo. Chigawochi chitithandiza kudziwa kuti Yehova amaona zimene timasankha ndipo sadzalola kuti choipa chigonjetse chabwino.