Munthu wina wosayenda ankakhala pakhomo la kachisi n’kumapemphapempha. Tsiku lina madzulo, munthuyo anaona Petulo ndi Yohane akulowa m’kachisimo. Iye anati: ‘Ndithandizeni!’ Petulo anamuyankha kuti: ‘Ndikupatsa chinthu chabwino kwambiri kuposa ndalama. M’dzina la Yesu dzuka n’kuyamba kuyenda.’ Kenako anamugwira n’kumudzutsa ndipo anayambadi kuyenda. Anthu anasangalala koopsa moti ambiri anakhala ophunzira.

Koma ansembe ndi Asaduki anakwiya kwambiri. Iwo anagwira atumwiwo n’kupita nawo kukhoti ndipo anakawafunsa kuti: ‘Mphamvu yochiritsira munthuyu mwaitenga kuti?’ Petulo anati: ‘Yesu amene munamupha uja ndi amene watipatsa.’ Ndiyeno atsogoleri achipembedzo ananena mokalipa kuti: ‘Musiyiretu kunena za Yesu.’ Koma atumwiwo anayankha kuti: ‘Ife sitisiya ndipo tizinenabe.’

Petulo ndi Yohane atangomasulidwa, anapita kwa ophunzira ena kukawauza zimene zinachitika. Iwo anapemphera limodzi kuti: ‘Chonde Yehova tithandizeni kuti tikhale olimba mtima kuti tizilalikirabe.’ Yehova anawapatsa mzimu woyera ndipo anapitiriza kulalikira ndi kuchiritsa anthu. Anthu ambiri anakhala ophunzira. Koma Asaduki zinkawapwetekabe moti anamanga atumwiwo n’kuwatsekera m’ndende. Ndiyeno Yehova anatumiza mngelo usiku kuti akatsegule zitseko za ndendeyo n’kuuza atumwiwo kuti: ‘Bwererani kukachisi muzikaphunzitsa anthu.’

Tsiku lotsatira, Khoti Lalikulu la Ayuda linauzidwa kuti: ‘Zitseko za ndende n’zotseka koma anthu aja apita. Panopa ali kukachisi ndipo akuphunzitsa anthu.’ Anthu anapita kukawamanganso n’kupita nawo ku Khoti Lalikulu la Ayuda. Atafika, mkulu wa ansembe anati: ‘Kodi sitinakuuzeni kuti musiye kunena  za Yesu?’ Koma Petulo anayankha kuti: “Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.”

Atsogoleri achipembedzo anakwiya kwambiri moti ankafuna kupha atumwiwo. Koma Mfarisi wina dzina lake Gamaliyeli anaimirira n’kunena kuti: ‘Anthu inu samalani. Anthuwatu ayenera kuti akuthandizidwa ndi Mulungu. Kodi mukufuna kulimbana ndi Mulungu?’ Anthuwo anamvera mawu ake moti anangowakwapula n’kuwauza kuti azipita koma asakalalikirenso. Koma atumwiwo sanasiye kulalikira. Iwo ankalalikirabe mwakhama m’kachisi komanso kunyumba ndi nyumba.

“Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.”​—Machitidwe 5:29