Akhristu oyambirira analalikira uthenga wabwino wa Ufumu m’madera ambiri padzikoli. Yesu ankawatsogolera kuti adziwe kokalalikira ndiponso anawathandiza kulalikira m’zilankhulo zina. Yehova anawathandizanso kuti akhale olimba mtima komanso anawapatsa mphamvu kuti azipirira akamazunzidwa.

Yesu anaonetsa mtumwi Yohane masomphenya a ulemerero wa Yehova. M’masomphenya ena anamuonetsa Ufumu wakumwamba ukugonjetsa Satana ndiponso kumuchititsa kuti asamasocheretsenso anthu. Yohane anaona Yesu akulamulira limodzi ndi anthu 144,000. Anaonanso dziko lonse lili Paradaiso komanso anthu onse akulambira Yehova mogwirizana.