Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo

 MUTU 93

Yesu Anabwerera Kumwamba

Yesu Anabwerera Kumwamba

Yesu ndi ophunzira ake anakumana ku Galileya. Kumeneko anawapatsa lamulo lofunika kwambiri lakuti: ‘Pitani mukaphunzitse anthu a m’mayiko onse kuti akhale ophunzira anga. Mukawaphunzitse zimene ndinakuphunzitsani ndipo mukawabatize.’ Kenako anawalonjeza kuti: ‘Ndikhala nanu limodzi.’

Yesu ataukitsidwa anakhala padzikoli masiku 40 ndipo anaonana ndi ophunzira ake ambiri ku Galileya ndi ku Yerusalemu. Anawaphunzitsa zinthu zambiri komanso anachita zodabwitsa. Kenako anakumana ndi atumwi ake komaliza paphiri la Maolivi. Anawauza kuti: ‘Musachoke mu Yerusalemu. Mudikire zimene Atate analonjeza.’

Atumwi akewo sanamvetse zimene Yesu ankatanthauza. Moti anamufunsa kuti: ‘Kodi tsopano mukhala Mfumu ya Aisiraeli?’ Koma iye anawayankha kuti: ‘Nthawi ya Mulungu yoti ndikhale Mfumu sinakwane. Mudzalandira mphamvu ya mzimu ndipo mudzakhala mboni zanga. Mudzaphunzitsa anthu ku Yerusalemu, ku Yudeya, ku Samariya mpaka kumalekezero a dziko.’

Kenako Yesu anayamba kukwera kumwamba ndipo anabisika m’mitambo. Atumwi akewo ankangoyang’anabe m’mwamba mpaka Yesu anabisika.

Ndiyeno atumwiwo anachoka paphiri la Maolivi n’kupita ku Yerusalemu. Nthawi zonse ankakumana m’chipinda chapamwamba n’kumapemphera. Ankadikira kuti Yesu awapatse malangizo ena.

“Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”​—Mateyu 24:14