Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo

 MUTU 84

Yesu Anayenda Panyanja

Yesu Anayenda Panyanja

Kuwonjezera pa kuchiritsa odwala ndi kuukitsa akufa, Yesu ankathanso kulamulira mphepo komanso mvula. Tsiku lina, Yesu atamaliza kupemphera m’phiri anaona kuti panyanja ya Galileya panali chimphepo ndi mafunde. Atumwi ake anali m’boti ndipo ankalimbana ndi mphepo panyanjapo. Ndiyeno iye anatsika m’phirimo n’kuyamba kuyenda pamadzi kupita kumene kunali boti la atumwi akewo. Atumwiwo ataona munthu akuyenda pamadzi, anachita mantha. Koma Yesu anawauza kuti: ‘Musaope, ndine.’

Petulo anati: ‘Ambuye ngati ndinuyo, ndiuzeni ndibwere kumene muliko.’ Yesu anamuuza kuti: ‘Bwera.’ Choncho Petulo anatuluka m’boti muja n’kuyamba kuyenda pamadzi kupita kumene kunali Yesu. Koma atayandikira, anayang’ana chimphepo chija. Atatero anachita mantha ndipo anayamba kumira. Iye anafuula kuti: ‘Ambuye, ndithandizeni!’ Yesu anamugwira dzanja n’kumufunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani unayamba kukayikira? Chikhulupiriro chako chili kuti?’

Yesu ndi Petulo anakwera m’boti muja ndipo nthawi yomweyo mphepo ija inasiya. Kodi ukuganiza kuti atumwiwo anamva bwanji? Iwo anati: “Ndinudi Mwana wa Mulungu.”

Si nthawi yokhayi pamene Yesu anachita zodabwitsa ngati zimenezi. Pa nthawi ina ali ndi atumwi ake muboti, Yesu anapita chakumbuyo kwa botilo n’kugona. Iye ali m’tulo, panyanjapopanayambika chimphepo. Mafunde ankamenya botilo ndipo mubotilo munalowa madzi. Atumwi anamudzutsa n’kumuuza kuti: ‘Mphunzitsi tifatu, chonde tithandizeni.’ Yesu anadzuka n’kuuza nyanjayo kuti: “Leka! Khala bata!” Nthawi yomweyo chimphepo chija chinatha ndipo panyanjapo panali bata. Ndiyeno Yesu anafunsa atumwiwo kuti: “Chikhulupiriro chanu chili kuti?” Atumwiwo anayamba kuuzana kuti : “Ngakhale mphepo ndi nyanja zikumumvera.” Iwo anaphunzirapo kuti ngati amakhulupirira kwambiri Yesu, sayenera kuopa chilichonse.

“Ngati ndikanakhala wopanda chikhulupiriro poona ubwino wa Yehova m’dziko la anthu amoyo, ndikanataya chiyembekezo.”​—Salimo 27:13