Yesu anaphunzitsa anthu zokhudza Ufumu wakumwamba. Iye anawaphunzitsanso kuti azipemphera kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe, Ufumu wake ubwere komanso chifuniro chake chichitike padzikoli. Ngati ndinu kholo, fotokozerani mwana wanuyo chifukwa chake pempheroli ndi lofunika kwa ife. Yesu sanalole kuti Satana amulepheretse kukhala wokhulupirika kwa Mulungu. Iye anasankha atumwi ake ndipo iwo ndi amene anali oyamba kusankhidwa kuti adzalamulire nawo mu Ufumu. Ngati ndinu kholo, thandizani mwana wanuyo kuti aone zoti Yesu anali wodzipereka kwambiri pa kulambira koona. Popeza Yesu ankafuna kuthandiza anthu anachiritsa odwala, anadyetsa anjala komanso anaukitsa akufa. Zinthu zodabwitsa zimene anachitazi zinasonyeza zimene Ufumu wa Mulungu udzachitire anthu.