Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo

 MUTU 70

Angelo Analengeza za Kubadwa kwa Yesu

Angelo Analengeza za Kubadwa kwa Yesu

Pa nthawi ina mu ulamuliro wa Kaisara Augusito, panaperekedwa lamulo loti Ayuda onse abwerere m’mizinda ya kwawo kuti akalembetse m’kaundula. Yosefe ndi Mariya anapita ku Betelehemu komwe kunali kwawo kwa Yosefe. Apa n’kuti Mariya atatsala pang’ono kubereka.

Atafika ku Betelehemu, anapeza kuti nyumba zonse ndi zodzaza moti anagona m’khola. Zimenezi zinachititsa kuti Yesu anabadwire m’kholamo. Mariya anakulunga mwanayo ndi nsalu zabwino n’kumugoneka modyetsera ziweto.

Pa nthawiyo, abusa ena ankagona kutchire pafupi ndi ku Betelehemu n’kumayang’anira nkhosa zawo. Mwadzidzidzi, mngelo anafika ndipo pamalo onsewo panawala kusonyeza ulemerero wa Yehova. Abusawo anachita mantha koma mngeloyo anati: ‘Musaope. Ndabwera ndi uthenga wosangalatsa. Lero Mesiya wabadwa ku Betelehemu.’ Nthawi yomweyo,  angelo ambirimbiri anaoneka m’mlengalenga ndipo ankanena kuti: ‘Alemekezeke Mulungu kumwamba ndipo mtendere ukhale padziko lapansi.’ Kenako angelowo sanaonekenso. Kodi ukudziwa zimene abusawo anachita?

Anauzana kuti: ‘Tiyeni ku Betelehemu pompanopompano.’ Nthawi yomweyo ananyamuka ndipo atafika anaona Yosefe ndi Mariya ali ndi kamwana kawo m’khola.

Aliyense amene anamva zimene angelowo anauza abusawo anadabwa kwambiri. Mariya anaganizira kwambiri mawu a angelowo ndipo sanawaiwale. Abusawo anabwerera kutchire kuja uku akuthokoza Yehova chifukwa cha zonse zimene anaona.

“Ine ndinachokera kwa Mulungu ndipo ndili pano. Sindinabwere mwakufuna kwanga ayi, koma Iyeyo anandituma.”​—Yohane 8:42

Onaninso

TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO

‘Anaganizira Tanthauzo la Mawu Onsewo Mumtima Mwake’

Zimene Mariya anaona ndiponso kumva ali ku Betelehemu zinamuthandiza kukhulupirira kwambiri malonjezo a Yehova.

YESU—NDI NJIRA, CHOONADI NDI MOYO

Yesu Analemekezedwa Asanabadwe

Kodi Elizabeti komanso mwana amene anali m’mimba mwake analemekeza bwanji Yesu?

YESU—NDI NJIRA, CHOONADI NDI MOYO

Kodi Yesu Anabadwa Liti Ndipo Anabadwira Kuti?

Kodi timadziwa bwanji kuti Yesu sanabadwe pa 25 December?

MOVIES

“Mulungu Anamuika Kukhala Ambuye Ndi Khristu”

Mkhristu akhoza kuyamba kukaikira ndipo chikhulupiriro chake chingayambe kufooka. Kuonera vidiyoyi kukuthandizani kuti muzikhulupira kwambiri Yesu, amene ndi Mesiya wolonjezedwa komanso Mfumu ya Ufumu wa Mulungu.