Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo

 MUTU 60

Ufumu Umene Udzalamulire Mpaka Kalekale

Ufumu Umene Udzalamulire Mpaka Kalekale

Tsiku lina usiku, Nebukadinezara analota maloto odabwitsa. Malotowo anamuvutitsa kwambiri moti sanagonenso. Kenako anaitana amatsenga ake n’kuwauza kuti: ‘Tandiuzeni, ndalota chiyani ine.’ Amatsengawo anati: ‘Inuyo mutiuze zimene mwalota ndipo ifeyo tikuuzani tanthauzo lake.’ Koma Nebukadinezara anati: ‘Ayi. Inuyo mundiuze zimene ndalota, apo ayi ndikuphani.’ Iwo anamuuzanso kachiwiri kuti: ‘Tangotiuzani malotowo ndipo ife tikuuzani tanthauzo lake.’ Iye anati: ‘Nonsenu mukungofuna kundipusitsa. Tanenani. Ndalota chiyani?’ Iwo anamuyankha kuti: ‘Palibetu munthu amene angadziwe zimene mwalota. Zimenezo n’zosatheka.’

Nebukadinezara anakwiya kwambiri moti analamula kuti amuna onse anzeru aphedwe. Apa ndiye kuti nayenso Danieli, Sadirake, Mesake ndi Abedinego akanaphedwa. Danieli atamva zimenezi anapempha mfumu kuti imupatse nthawi kuti aone zimene angachite. Kenako iye ndi anzakewo anapemphera kwa Yehova kuti awathandize. Ndiye kodi Yehova anatani?

Kudzera m’masomphenya, Yehova anauza Danieli maloto a Nebukadinezara komanso tanthauzo lake. Tsiku lotsatira Danieli anapita kwa atumiki a mfumu n’kuwauza kuti: ‘Musaphe munthu aliyense. Ine ndikauza mfumu maloto ake.’ Atumikiwo anamutenga n’kupita naye kwa mfumu. Kumeneko Danieli anauza mfumu kuti: ‘Mulungu wakudziwitsani zimene zidzachitike m’tsogolo. Zimene munalota ndi izi: Munaona chifaniziro chachikulu. Mutu wake unali wagolide, chifuwa ndi manja ake zinali zasiliva, mimba ndi ntchafu zinali zamkuwa, miyendo yake inali yachitsulo ndipo mapazi ake anali achitsulo chosakanizika ndi dongo. Kenako mwala unadulidwa kuphiri ndipo unamenya mapazi a chifanizirocho. Chifanizirocho chinaphwanyika n’kusanduka fumbi lomwe linauluzika ndi mphepo. Ndiyeno mwala uja unakula n’kukhala phiri lalikulu ndipo linadzaza padziko lonse lapansi.’

 Kenako Danieli anati: ‘Tanthauzo la maloto anuwa ndi ili: Ufumu wanu ndiye mutu wagolidewo. Siliva akuimira ufumu womwe udzabwere pambuyo panu. Kenako udzabwera ufumu wina wangati mkuwa umenenso udzalamulire padziko lonse. Pambuyo pa umenewo padzabwera ufumu wolimba ngati chitsulo. Pomaliza padzabwera ufumu wogawanika, mbali zake zina zidzakhala zolimba ngati chitsulo koma zina zidzakhala zosalimba ngati dongo. Mwala umene unakula n’kukhala phiri, ukuimira Ufumu wa Mulungu. Ufumuwu udzaphwanya maufumu onse ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.’

Nebukadinezara atamva zimenezi anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi. Kenako anati: ‘Mulungu wako ndi amene wakuululira malotowa. Palibenso Mulungu wina wofanana naye.’ Nebukadinezara anapatsa Danieli udindo woti aziyang’anira anthu onse anzeru. Anamuikanso kukhala wolamulira chigawo chonse cha Babulo. Kodi waona mmene Yehova anayankhira pemphero la Danieli?

“Anawasonkhanitsa pamodzi, kumalo amene m’Chiheberi amatchedwa Haramagedo.”​—Chivumbulutso 16:16