Esitere anali mtsikana wachiyuda ndipo ankakhala mumzinda wa Susani ku Perisiya. Banja lawo linatengedwa ndi Nebukadinezara kuchokera ku Yerusalemu. Ndiyeno ku Perisiyako ankaleredwa ndi wachibale wake, dzina lake Moredekai, yemwe ankagwira ntchito kwa Mfumu Ahasiwero.

Pa nthawi ina, Mfumu Ahasiwero ankafuna mfumukazi yatsopano. Ndiyeno atumiki ake anamubweretsera akazi onse okongola a m’dzikolo. Esitere analinso gulu lomweli. Mfumuyo inasankha Esitere kuti akhale mfumukazi. Koma Moredekai anauza Esitere kuti asaulule zoti iye ndi Myuda.

M’dzikolo munali munthu wina dzina lake Hamani. Iye ankayang’anira nduna za mfumu koma anali wonyada kwambiri ndipo ankafuna kuti aliyense azimuweramira. Koma Moredekai sankaweramira Hamani. Choncho Hamani anakwiya kwambiri moti ankafuna kupha Moredekai ndipo atamva zoti Moredekai ndi Myuda, anakonza zoti aphe Ayuda onse. Anauza mfumu kuti: ‘Ayudatu ndi anthu oopsa kwambiri moti muyenera kuwapha onse.’ Zitatero inamupatsa mphamvu yokonza lamulo ndipo inamuuza kuti: ‘Chita chilichonse chimene ukuona kuti chithandiza.’ Hamani anakonza lamulo louza anthu kuti aphe Ayuda onse pa tsiku la 13 la mwezi wa Adara. Koma Yehova ankaona zonsezi.

Esitere sankadziwa za lamuloli. Choncho Moredekai anamutumizira chikalata chonena za lamuloli komanso uthenga wakuti: ‘Pita ukalankhule ndi mfumu za nkhaniyi.’ Esitere anati: ‘Aliyense wopita kwa mfumu asanaitanidwe, amaphedwa. Patha masiku 30 mfumu isanandiitane. Koma ndipitabe. Akakandiloza ndi ndodo, ndiye kuti sindiphedwa. Koma akakapanda kutero ndiye kuti ndikaphedwa.’

Esitere anapitadi kwa mfumu ndipo inamuloza ndi ndodo. Kenako inamufunsa kuti: ‘Esitere, ukufuna ndikuchitire chiyani?’ Esitere anayankha kuti: ‘Ndikupempha kuti inuyo ndi Hamani mubwere kuphwando limene ndikonze.’ Atapita kuphwandolo,  anawapempha kuti abwerenso tsiku lotsatira. Pa ulendo wachiwiriwu, mfumu inafunsanso Esitere kuti: ‘Ukufuna ndikuchitire chiyani?’ Iye anayankha kuti: ‘Pali munthu wina amene akufuna kupha ineyo komanso anthu a mtundu wanga. Chonde, tipulumutseni.’ Mfumuyo inafunsa kuti: ‘Ndani akufuna kukuphani?’ Iye anati: ‘Ndi Hamani woipa ali apayu.’ Ahasiwero anakwiya kwambiri moti analamula kuti Hamani aphedwe nthawi yomweyo.

Komano panalibe munthu aliyense amene akanafafaniza lamulo lija. Choncho mfumuyo inasankha Moredekai kuti akhale mkulu wa nduna zake ndipo anamupatsa mphamvu yokonza lamulo latsopano. Ndiyeno Moredekai anakonza lamulo lopatsa Ayuda mphamvu kuti adziteteze. Tsiku la 13 la mwezi wa Adara litafika, Ayuda anadziteteza kwa adani awo ndipo anawagonjetsa. Kuchokera pa nthawiyi Ayuda anayamba kukondwerera tsiku limeneli chaka chilichonse.

“Adzakutengerani kwa abwanamkubwa ndi mafumu chifukwa cha ine, kuti ukhale umboni kwa iwo ndi kwa anthu a mitundu ina.”​—Mateyu 10:18