Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo

 MUTU 63

Dzanja Linalemba Pakhoma

Dzanja Linalemba Pakhoma

Patapita nthawi, Belisazara anakhala mfumu ya Babulo. Tsiku lina madzulo anakonza phwando ndipo anaitana nduna zake zokwana 1,000. Kenako anauza atumiki ake kuti akatenge makapu agolide amene Nebukadinezara anatenga m’kachisi wa Yehova. Iye ndi nduna zakezo anayamba kumwera vinyo m’makapuwo n’kumatamanda milungu yawo. Koma mwadzidzidzi, anangoona dzanja la munthu likulemba mawu odabwitsa pakhoma la m’chipinda chimene ankachitira phwandolo.

Belisazara anachita mantha kwambiri. Anaitana anthu a matsenga n’kuwauza kuti: ‘Aliyense amene angandiuze tanthauzo la mawuwa, ndimuika kukhala wolamulira wachitatu mu ufumu wa Babulo.’ Koma palibe anatha kumuuza tanthauzo la mawuwo. Kenako mkazi wake anabwera n’kudzamuuza kuti: ‘Pali munthu wina dzina lake Danieli amene ankauza Nebukadinezara tanthauzo la zinthu zosiyanasiyana. Akhozatu kukuuzani tanthauzo la mawuwa.’

Danieli atafika, Belisazara anamuuza kuti: ‘Ngati ungathe kuwerenga mawuwa n’kundiuza kumasulira kwake, ndikupatsa mkanda wagolide komanso ndikuika kuti ukhale wolamulira wachitatu mu ufumuwu.’ Koma Danieli anayankha kuti: ‘Sindikufuna mphatso zanuzo. Komabe ndikuwerengerani mawuwa ndiponso ndikuuzani kumasulira kwake. Bambo anu, a Nebukadinezara, anali odzikweza ndipo Yehova anawachepetsa. Inuyo mukudziwa zimene zinawachitikira, koma mukunyoza Yehova ndipo mukumwera vinyo m’makapu agolide a m’kachisi wake. Choncho Yehova walemba mawu awa: Mene, Mene, Tekeli ndi Parasini. Mawuwa akutanthauza kuti Amedi ndi Aperisiya adzagonjetsa Babulo ndipo inu simukhalanso mfumu.’

Pa nthawiyo zinkaoneka ngati palibe angagonjetse mzinda wa Babulo. Mzindawu unkaoneka kuti unali wotetezeka ndi mpanda wolimba komanso mtsinje waukulu. Koma usiku womwewo, Amedi ndi Aperisiya anaukira mzindawu. Mfumu ya Aperisiya, dzina lake Koresi, inapatutsa madzi a mumtsinje ndipo asilikali ake  anawoloka n’kukafika pageti la mzindawu. Atafika, anapeza kuti pagetipo m’posatseka. Choncho analowa n’kulanda mzindawo komanso kupha mfumu. Ndiyeno Koresi anayamba kulamulira Babulo.

Pasanathe chaka, Koresi ananena kuti: ‘Yehova wandiuza kuti ndimangenso kachisi wake wa ku Yerusalemu. Anthu ake amene akufuna kukathandiza nawo ntchitoyi, angathe kupita.’ Choncho mogwirizana ndi zimene Yehova analonjeza, Ayuda ambiri anabwerera ku Yerusalemu. Apa n’kuti patatha zaka 70 kuchokera pamene Yerusalemu anawonongedwa. Koresi anabwezeretsa makapu asiliva komanso zinthu zina zimene Nebukadinezara anatenga m’kachisi wa Yehova. Apatu Yehova anagwiritsa ntchito Koresi pothandiza anthu ake.

“Wagwa! Babulo Wamkulu wagwa, ndipo wakhala malo okhala ziwanda.”​—Chivumbulutso 18:2