Baibulo limayamba n’kufotokoza zokhudza chilengedwe ndipo izi zimatithandiza kuyamikira zinthu zokongola zimene Yehova analenga zakumwamba komanso zapadzikoli. Ngati ndinu kholo, thandizani mwana wanu kuti athe kuzindikira mfundo yoti Mulungu analenga zinthu zodabwitsa zosiyanasiyana. Fotokozani kuti Mulungu anatilenga anthufe mwapamwamba kusiyana ndi zinyama. Anatilenga kuti tizitha kulankhula, kuganiza, kupanga zinthu, kuimba komanso kupemphera. Muthandizeninso kudziwa kuti Yehova ali ndi mphamvu, nzeru komanso chikondi. Ndipo amakonda zolengedwa zake kuphatikizapo ifeyo, aliyense payekha.