MATEYU 3:1-12 MALIKO 1:1-8 LUKA 3:1-18 YOHANE 1:6-8, 15-28

  • YOHANE ANKALALIKIRA NDI KUBATIZA ANTHU

  • ANTHU AMBIRI ANABATIZIDWA KOMA OSATI ONSE

Pofika mu 29 C.E., n’kuti patadutsa zaka 17 kuchokera pamene Yesu ankafunsa mafunso aphunzitsi m’kachisi. Pa nthawi imeneyi anthu ambiri ankakambirana za wachibale wake wa Yesu, dzina lake Yohane, yemwe ankagwira ntchito yolalikira m’dera lonse lomwe linali chakumadzulo kwa mtsinje wa Yorodano.

Anthu ambiri ankachita chidwi kwambiri ndi Yohane chifukwa cha mmene ankaonekera komanso uthenga umene ankalalikira. Ankavala zovala zopangidwa ndi ubweya wa ngamila ndiponso ankavala lamba wachikopa m’chiuno mwake. Chakudya chake chinali dzombe ndi uchi. Koma kodi ankalalikira uthenga wotani? Unali wakuti: “Lapani, pakuti ufumu wakumwamba wayandikira.”—Mateyu 3:2.

Uthengawu unkafika pamtima anthu amene ankabwera kudzamvetsera. Anthu ambiri anazindikira kuti ankafunika kusintha zochita zawo komanso mmene ankaganizira ndipo anasiya zoipa zimene ankachita. Anthuwa ankachokera ku “Yerusalemu ndi ku Yudeya konse ndiponso . . . m’midzi yonse yapafupi ndi Yorodano.” (Mateyu 3:5) Anthu ambiri amene ankamvetsera uthenga wa Yohane analapa ndipo anawabatiza powamiza m’madzi, mumtsinje wa Yorodano. N’chifukwa chiyani ankawabatiza?

Ubatizowo unali ngati chizindikiro chakuti kuchokera pansi pamtima alapa machimo awo omwe anawachita chifukwa chosamvera Chilamulo cha Mulungu, chomwe chinali pangano pakati pa iwowo ndi Mulungu. (Machitidwe 19:4) Koma si onse amene anabatizidwa. Mwachitsanzo Afarisi ndi Asaduki atapita kukaona Yohane, iye anawatchula kuti “ana a njoka.” Iye ananenanso kuti: “Ndiyetu mubale zipatso zosonyeza kulapa. Musamadzinyenge kuti, ‘Tili ndi atate wathu Abulahamu.’ Pakuti ndikukuuzani kuti Mulungu angathe kuutsira Abulahamu ana kuchokera kumiyala iyi. Nkhwangwa yaikidwa kale pamizu yamitengo. Chotero mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino udulidwa ndi kuponyedwa pamoto.”—Mateyu 3:7-10.

Chifukwa chakuti uthenga wa Yohane unali wamphamvu ndipo anthu ambiri anakhulupirira komanso kubatizidwa, ansembe ndi Alevi anatumidwa kuti akafufuze kuti Yohaneyo anali ndani. Iwo anamufunsa kuti: “Kodi iwe ndiwe ndani?”

Yohane anawayankha kuti: “Ine sindine Khristu ayi.”

Anamufunsanso kuti: “Nanga ndiwe ndani? Ndiwe Eliya kapena?”

Iye anati: “Iyayi.”

Kenako anamufunsa kuti: “Kapena ndiwe Mneneri?” Apa ankafunsa za Mneneri amene Mose ananena kuti adzabwera.—Deuteronomo 18:15, 18.

Iye anayankha kuti: “Ayi.”

Analimbikirabe kumufunsa kuti: “Ndiwe ndani nanga? Tikufuna kudziwa kuti tikathe kupereka yankho kwa amene atituma. Mwiniwakewe umati ndiwe ndani?” Iye anati: “Ndine mawu a winawake wofuula m’chipululu kuti, ‘Wongolani njira ya Yehova,’ monga mmene mneneri Yesaya ananenera.”—Yohane 1:19-23.

Ndiyeno anamufunsa kuti: “Ngati iweyo sindiwe Khristu, kapena Eliya, kapenanso Mneneri, nanga n’chifukwa chiyani umabatiza anthu?” Yohane anawayankha kuti: “Ine ndimabatiza m’madzi. Pakati panu paimirira wina amene inu simukumudziwa. Iye ndiye amene akubwera m’mbuyo mwangamu.”—Yohane 1:25-27.

Pa nthawiyi, Yohane ankadziwa kuti akukonza njira pokonzekeretsa mitima ya anthuwo kuti adzathe kulandira Mesiya, amene anali kudzakhala Mfumu. Pofotokoza za Mesiyayo, Yohane ananena kuti: “Amene akubwera m’mbuyo mwanga ndi wamphamvu kuposa ine, ndipo sindili woyenera kumuvula nsapato zake.” (Mateyu 3:11) Yohane ananenanso kuti: “Amene akubwera m’mbuyo mwangamu wandipitirira ine, chifukwa anakhalapo ine ndisanabadwe.”—Yohane 1:15.

Choncho, uthenga umene Yohane ankalalikira wakuti: “Lapani, pakuti ufumu wakumwamba wayandikira,” unali woyenereradi. (Mateyu 3:2) Uthengawu unathandiza anthu onse kudziwa kuti ntchito imene Yesu Khristu anabwerera pa dziko lapansi inali itatsala pang’ono kuyamba.