LUKA 1:21-39

  • YESU ANADULIDWA KENAKO ANAPITA NAYE KU KACHISI

Yosefe ndi Mariya anakhalabe ku Betelehemu m’malo mobwerera kwawo ku Nazareti. Atatha masiku 8, Yesu anadulidwa potsatira zimene Chilamulo cha Mulungu chinkanena. (Levitiko 12:2, 3) Pa nthawiyo unali mwambo kuti mwana wamwamuna azipatsidwanso dzina pa tsiku limeneli. Choncho, anapatsa mwana wawo dzina lakuti Yesu potsatira zimene mngelo uja anawauza.

Kenako patatha masiku 40, Yosefe ndi Mariya anapita ndi Yesu kukachisi ku Yerusalemu. Kuchokera ku Betelehemu kupita kukachisiko unali ulendo wa makilomita ochepa. Iwo anapita kukachisiko chifukwa chakuti Chilamulo chinkanena kuti pakadutsa masiku 40 kuchokera pamene mkazi wabereka mwana wamwamuna, mkaziyo azikapereka nsembe kukachisi n’cholinga choti ayeretsedwe.—Levitiko 12:4-8.

Pokapereka nsembeyo, Mariya anatenga timbalame tiwiri. Zimenezi zikutithandiza kudziwa mmene zinthu zinalili pa moyo wawo. Chilamulo chinkanena kuti munthu azipereka mwana wa nkhosa ndi mbalame ngati nsembe yoyeretsa. Koma ngati mkaziyo sakwanitsa kupereka mwana wa nkhosayo, azipereka njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda. Ndipo izi n’zimene Mariya anachita chifukwa anali wosauka.

Ali kukachisiko munthu wina wachikulire dzina lake Simiyoni, anafika pamene panali Yosefe ndi Mariya. Mulungu anali atamuululira kuti asanamwalire adzaona Khristu, yemwe ndi Wodzozedwa wa Yehova kapena kuti Mesiya. Pa tsiku limeneli mzimu woyera unatsogolera Simiyoni kuti apite kukachisi kumene anakapeza Yosefe ndi Mariya komanso Yesu ali wakhanda. Kenako Simiyoni ananyamula mwanayo.

Atamunyamula, Simiyoni anathokoza Mulungu kuti: “Tsopano, Ambuye Wamkulu Koposa, mukulola kapolo wanu kupita mu mtendere malinga ndi zimene inu munanena. Chifukwa maso anga aona njira yanu yopulumutsira imene mwakonzeratu pamaso pa mitundu yonse ya anthu. Maso anga aona kuwala kochotsa nsalu yophimba mitundu ya anthu ndi ulemerero wa anthu anu Aisiraeli.”—Luka 2:29-32.

Atamva zimenezi, Yosefe ndi Mariya anadabwa kwambiri. Simiyoni anawadalitsa ndipo anauza Mariya kuti mwana wakeyo “waikidwa kuti ambiri agwe, ndiponso kuti ambiri adzukenso mu Isiraeli.” Anamuuzanso kuti chisoni chachikulu ngati lupanga lalitali chidzalasa moyo wake.—Luka 2:34.

Munthu wina amene analinso kukachisiko ndi Anna, mneneri wamkazi wazaka 84. Iye ankapezeka pakachisi nthawi zonse. Nayenso anapita pamene panali Yosefe ndi Mariya n’kuyamba kuthokoza Mulungu komanso kulankhula zokhudza Yesu kwa anthu ena omwe analipo.

Yosefe ndi Mariya ayenera kuti anasangalala kwambiri ndi zimene zinachitikazi ndipo zinawatsimikizira kuti mwana wawo analidi amene Mulungu analonjeza kuti adzabadwa.