Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 16

Yesu Anali Wodzipereka pa Kulambira Mulungu

Yesu Anali Wodzipereka pa Kulambira Mulungu

YOHANE 2:12-22

  • YESU ANAYERETSA KACHISI

Atachoka ku ukwati wa ku Kana, Yesu analowera ku Kaperenao. Pa ulendowu Yesu anali ndi mayi ake komanso abale ake omwe mayina awo anali Yakobo, Yosefe, Simoni ndi Yuda.

Koma n’chifukwa chiyani Yesu anapita ku Kaperenao? Mzinda wa Kaperenao unali waukulu komanso wodziwika kuposa mzinda wa Nazareti kapena wa Kana. Komanso ophunzira ambiri a Yesu ankakhala mumzinda umenewu kapena chakufupi ndi mzindawu ndipo Yesu akanatha kuwaphunzitsa zinthu zina ali kwawo.

Pa nthawi imene Yesu anali ku Kaperenao anachita zinthu zozizwitsa. Choncho anthu ambiri a mumzindawu ndi madera ena ozungulira anamva zimene Yesu anachita kumeneko. Koma Yesu ndi ophunzira ake, omwe anali Ayuda odzipereka, sanakhalitse mumzindawo. Iwo ananyamuka kupita ku Yerusalemu kuti akachite nawo mwambo wa Pasika wa mu 30 C.E.

Atafika kukachisi ku Yerusalemu, ophunzirawo anaona Yesu akuchita zinthu zodabwitsa kwambiri zimene anali asanachitepo.

Pa nthawiyi Chilamulo cha Mulungu chinkanena kuti Aisiraeli azipereka nsembe za nyama pakachisi. Koma panali anthu ena omwe ankachokera kutali omwe ankafunika kugula zakudya komanso zinthu zina zofunikira pa nthawi yonse imene ankakhala ku Yerusalemuko. Choncho Chilamulo chinkalola anthu amenewa kubweretsa ndalama zimene ankagulira “ng’ombe, nkhosa, mbuzi,” komanso zinthu zina. (Deuteronomo 14:24-26) Chifukwa cha zimenezi, amalonda a ku Yerusalemu ankagulitsa nyama kapena mbalame mkati mwa bwalo la kachisiyo, zimene anthu ankapereka nsembe. Ena mwa amalondawa ankabera anthu powagulitsa zinthuzi pa mtengo wokwera kwambiri.

Yesu ataona zimenezi anakwiya kwambiri ndipo anakhuthula makobidi a osintha ndalama, kugubuduza matebulo awo n’kuwathamangitsa. Kenako Yesu anauza anthuwo kuti: “Chotsani izi muno! Mulekeretu kusandutsa nyumba ya Atate wanga kukhala nyumba ya malonda.”—Yohane 2:16.

Ophunzira a Yesu ataona zimenezi anakumbukira ulosi wonena za Mwana wa Mulungu womwe unanena kuti: “Kudzipereka kwambiri panyumba yanu kudzandidya.” Koma Ayuda anafunsa kuti: “Utionetsa chizindikiro chotani tsopano chosonyeza kuti uli ndi ulamuliro wochitira zinthu zimenezi?” Yesu anayankha kuti: “Gwetsani kachisi uyu, ndipo ine ndidzamumanga m’masiku atatu.”—Yohane 2:17-19; Salimo 69:9.

Ayuda ankaganiza kuti Yesu ankanena za kachisi weniweni amene anali ku Yerusalemu, choncho anafunsa kuti: “Kachisi ameneyu anamumanga zaka 46, ndiye iwe udzamumanga m’masiku atatu?” (Yohane 2:20) Koma Yesu ankanena za thupi lake lomwe linali ngati kachisi. Patapita zaka zitatu kuchokera pa nthawiyi, ophunzira ake anakumbukira mawu amenewa Yesu ataukitsidwa.