Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo

 MUTU 17

Yesu Anaphunzitsa Nikodemo

Yesu Anaphunzitsa Nikodemo

YOHANE 2:23–3:21

  • YESU ANACHEZA NDI NIKODEMO

  • KODI “KUBADWANSO” KUMATANTHAUZA CHIYANI?

Pamene Yesu anali ku Yerusalemu ku mwambo wa Pasika m’chaka cha 30 C.E., anachita zinthu zodabwitsa moti anthu ambiri anayamba kumukhulupirira. Mwachitsanzo, munthu wina dzina lake Nikodemo, yemwe anali Mfarisi komanso woweruza wa m’khoti lalikulu la Ayuda lomwe linkadziwikanso kuti Sanihedirini, anachita chidwi kwambiri ndi zimene Yesu ankaphunzitsa ndipo ankafuna kudziwa zambiri. Kutada anapita kukakumana ndi Yesu. N’kutheka kuti anachita zimenezi chifukwa choopa kuti mbiri yake ingaipe ngati atsogoleri ena Achiyuda atadziwa za nkhaniyi.

Nikodemo atakumana ndi Yesu ananena kuti: “Rabi, tikudziwa kuti inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu, chifukwa munthu sangathe kuchita zizindikiro zimene inu mumachita ngati Mulungu sali naye.” Poyankha Yesu anauza Nikodemo kuti ngati munthu akufuna kulowa mu Ufumu wa Mulungu ayenera “kubadwanso.”—Yohane 3:2, 3.

Pofuna kudziwa kuti zingatheke bwanji kuti munthu abadwenso, Nikodemo anafunsa kuti: “Kodi angathe kulowa m’mimba mwa mayi ake ndi kubadwanso?”—Yohane 3:4.

Kubadwanso sikutanthauza zimenezi. Yesu anafotokoza kuti: “Munthu sangathe kulowa mu ufumu wa Mulungu atapanda kubadwa mwa madzi ndi mzimu.” (Yohane 3:5) Pa nthawi imene Yesu ankabatizidwa, mzimu woyera unatsika n’kutera pa iye, choncho pa nthawiyi iye anabadwanso “mwa madzi ndi mzimu.” Zimenezi zitangochitika, panamveka mawu ochokera kumwamba akuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.” (Mateyu 3:16, 17) Mulungu anachita zimenezi posonyeza kuti waberekanso Yesu kukhala mwana wake wauzimu n’kumupatsa chiyembekezo chodzalowa mu Ufumu wakumwamba. Kenako pa Pentekosite wa mu 33 C.E., anthu ena amene anali atabatizidwa analandira mzimu woyera ndipo anthu amenewa anabadwanso monga ana auzimu a Mulungu.—Machitidwe 2:1-4.

Nikodemo sanamvetse zimene Yesu anamuphunzitsa zokhudza Ufumu. Choncho Yesu anapitiriza kumufotokozera za udindo wapadera umene ali nawo monga Mwana wa Mulungu. Yesu anati: “Monga mmene Mose anakwezera njoka m’mwamba m’chipululu, momwemonso Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa m’mwamba, kuti aliyense wokhulupirira iye akhale nawo moyo wosatha.”—Yohane 3:14, 15.

Pa nthawi ina Aisiraeli ali m’chipululu, akalumidwa ndi njoka za poizoni, ankafunika kuyang’ana njoka ya mkuwa kuti akhale ndi moyo. (Numeri 21:9) Mofanana ndi zimenezi, anthu onse ayenera kukhulupirira Mwana wa Mulungu kuti adzapulumuke n’kupeza moyo wosatha. Pofotokoza zimene Yehova anachita kuti apulumutse anthu, Yesu anauza Nikodemo kuti: “Pakuti Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Ali ku Yerusalemuko ndi pamene Yesu ananena momveka bwino kuti iye ndi njira imene anthu angadzapulumikire. Pa nthawiyi n’kuti patapita miyezi 6 kuchokera pamene anayamba utumiki wake.

Yesu anauza Nikodemo kuti: “Mulungu anatumiza Mwana wake m’dziko, osati kuti mwanayo adzaweruze dziko.” Zimenezi sizikutanthauza kuti iye anabwera kuti adzaweruze anthu onse n’kuwapeza olakwa kuti alandire chilango. M’malomwake, monga mmene Yesu ananenera, iye anatumizidwa padzikoli “kuti mwa iye, dziko lipulumutsidwe.”—Yohane 3:17.

Nikodemo anapita kukakumana ndi Yesu usiku chifukwa cha mantha. N’zochititsa chidwi kuti Yesu anamaliza kukambirana kwawoko pomuuza kuti: “Tsopano maziko operekera chiweruzo ndi awa, kuwala [komwe kunkaimira zimene Yesu ankachita komanso zimene ankaphunzitsa] kwafika m’dziko koma anthu akonda mdima m’malo mwa kuwala, pakuti ntchito zawo n’zoipa. Amene amachita zinthu zoipa amadana ndi kuwala ndipo safika pamene pali kuwala, kuti  ntchito zake zisadzudzulidwe. Koma amene amachita chimene chili chabwino amabwera pamene pali kuwala, kuti ntchito zake zionekere kuti anazichita mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.”—Yohane 3:19-21.

Tsopano zinali kwa Nikodemo, yemwe anali Mfarisi komanso mphunzitsi wa Isiraeli, kuganizira mozama zimene Yesu anamuuza zokhudza udindo umene Yesuyo anali nawo pokwaniritsa cholinga cha Mulungu.