Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo

Njira, Choonadi ndi Moyo

Njira, Choonadi ndi Moyo

Aliyense amasangalala akalandira uthenga wabwino. Ndipotu pali uthenga wina wabwino wofunika kwambiri kwa inuyo komanso anthu amene mumawakonda.

Uthenga wabwinowu umapezeka m’Baibulo, lomwe ndi buku limene Yehova Mulungu, yemwe analenga kumwamba ndi dziko lapansi, anachititsa kuti lilembedwe zaka zambirimbiri zapitazo. M’buku lino tikambirana kwambiri za uthenga wabwino wopezeka m’mabuku 4 a m’Baibulo. Uthengawo ndi wothandiza kwa aliyense. Mulungu anagwiritsa ntchito Mateyu, Maliko, Luka ndi Yohane kulemba mabuku omwe ali ndi uthenga wabwinowu. Mabuku omwe anthuwa analemba amadziwikanso ndi mayina awo.

Anthu ambiri amatchula mabuku 4 a m’Baibulo amenewa kuti Mauthenga Abwino. Mabuku 4 onsewa amafotokoza uthenga wabwino wonena za Yesu, yemwe ndi Mfumu yosankhidwa ndi Mulungu, kuti ndi njira imene Mulungu anakonza yoti apulumutsire anthu. Amafotokozanso kuti Ufumu wa Mulungu womwe uli kumwamba udzabweretsa madalitso omwe sadzatha kwa anthu amene amakhulupirira Yesu.—Maliko 10:17, 30; 13:13.

N’CHIFUKWA CHIYANI PANAFUNIKA ANTHU 4 OLEMBA UTHENGA WABWINO?

Mwina munadzifunsapo kuti: N’chifukwa chiyani Mulungu anafuna kuti pakhale mabuku 4 ofotokoza za moyo wa Yesu komanso zimene ankaphunzitsa?

Kukhala ndi mabuku 4 ofotokoza zimene Yesu ankalankhula komanso zimene anachita n’kothandiza kwambiri. Kuti timvetse mfundo imeneyi tiyerekeze kuti pali mphunzitsi wina wodziwika kwambiri ndipo anthu 4 akhala pafupi ndi mphunzitsiyo. Munthu amene wakhala kutsogolo kwa mphunzitsiyu amagwira ntchito mu ofesi yokhometsera msonkho. Amene wakhala kumanja kwake ndi dokotala. Kumanzere kwake kwakhala munthu amene amagwira ntchito yopha nsomba komanso amagwirizana kwambiri ndi mphunzitsiyo. Munthu wanambala 4 wakhala kumbuyo kwake ndipo amachita chidwi kwambiri ndi zimene mphunzitsiyu amachita komanso ndi wamng’ono pa onsewo. Anthu onsewa amachita zinthu mwachilungamo komanso amachita chidwi ndi zinthu zosiyanasiyana. Ngati anthuwa atalemba zimene mphunzitsiyo walankhula komanso kuchita, ndiye kuti aliyense akhoza kufotokoza nkhaniyo mogwirizana ndi mmene waionera komanso mogwirizana ndi luso limene ali nalo. Choncho ngati titawerenga nkhani 4, zimene anthuwa alemba, tikhoza kumvetsa bwino zimene mphunzitsiyo ananena komanso kuchita. Zimenezi zikutithandiza kuona kuti mabuku 4 ofotokoza moyo wa Yesu, yemwe anali Mphunzitsi Waluso, ndi othandiza kwambiri.

Tikabwereranso ku chitsanzo chathu chija, munthu wogwira ntchito yokhometsa msonkho uja akufuna kuthandiza  Ayuda ndiye akamalemba nkhani zake akumazifotokoza kuti Ayuda asavutike kumva. Pomwe dokotala uja akufotokoza kwambiri za kuchiritsa anthu odwala kapena olumala ndipo akamafotokoza zinthu zina zomwe wokhometsa msonkho uja wazilemba kale, akusankha kusiya zinthu zina kapena kuzifotokoza mwanjira ina. Koma munthu amene amagwirizana kwambiri ndi mphunzitsi uja akufotokoza kwambiri makhalidwe komanso mmene mphunzitsiyo amaonera zinthu. Zimene akulemba zikumakhala zachidule komanso zomveka bwino. Onse akulemba nkhanizo mogwirizana ndi mmene zachitikira. Chitsanzo chimenechi chikusonyeza kuti kukhala ndi mabuku 4 amene akufotokoza zimene zinachitika pa moyo wa Yesu kumatithandiza kumvetsa bwino makhalidwe ake, zimene anachita komanso kuphunzitsa.

Anthu ena akamanena za buku la Mateyu kapena la Yohane amanena kuti ‘Uthenga wa Mateyu’ kapena ‘Uthenga wa Yohane’ koma zimenezi sizolondola. Tikutero chifukwa mabuku 4 onsewa ali ndi “uthenga wabwino wonena za Yesu Khristu.” (Maliko 1:1) Choncho mwachidule tinganene kuti m’mabuku onsewa muli uthenga wabwino umodzi wonena za Yesu.

Anthu ambiri amene akhala akuphunzira Mawu a Mulungu ayesapo kuyerekeza ndi kugwirizanitsa nkhani zimene zinalembedwa m’buku la Mateyu, Maliko, Luka ndi Yohane. Mwachitsanzo, chaka cha 170 C.E. chisanafike, munthu wina anayesapo kuchita zimenezi. Munthuyu anali wolemba mabuku wa ku Syria ndipo dzina lake anali Tatian. Iye anapeza kuti mabuku 4 amenewa amafotokoza nkhani molondola komanso kuti Mulungu ndi amene anachititsa kuti mabukuwa alembedwe. Zimene anapezazo zinamuchititsa kulemba buku la mutu wakuti Diatessaron, lomwe limagwirizanitsa mfundo za m’mabuku omwe amanena za moyo wa Yesu komanso zimene anachita pamene ankalalikira.

Buku lino, lomwe lili ndi mutu wakuti Yesu Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo, limagwirizanitsanso mfundo za m’mabuku omwe amafotokoza za moyo wa Yesu momveka bwino komanso molondola kwambiri. Zimenezi zili choncho chifukwa chakuti panopa tikutha kumvetsa bwino maulosi komanso mafanizo amene Yesu ananena. Zimenezi zimatithandiza kuti tizimvetsanso zimene ananena, kuchita komanso nthawi imene zinthuzo zinachitika. Zimene anthu amene amafukula zinthu zakale apeza zatithandizanso kumvetsa mfundo zina komanso mmene Mateyu, Maliko, Luka ndi Yohane ankaonera zinthu. Komabe palibe amene angakakamire maganizo ake pofotokoza mmene nkhani iliyonse inayendera. Koma bukuli likufotokoza zimene zinachitika pa moyo wa Yesu momveka bwino komanso motsatirika.

NJIRA, CHOONADI NDI MOYO

Mukamawerenga bukuli, yesetsani kupeza mfundo zimene zingathandize inuyo komanso zimene zingathandize anzanu. Pa nthawi ina Yesu Khristu anauza mtumwi Tomasi kuti: “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.”—Yohane 14:6.

Bukuli likuthandizani kumvetsa chifukwa chake tikunena kuti Yesu ndi “njira.” Anthufe timatha kupemphera kwa Yehova Mulungu kudzera mwa Yesu. Komanso chifukwa cha Yesu, anthufe timatha kugwirizananso ndi Mulungu. (Yohane 16:23; Aroma 5:8) Choncho kudzera mwa Yesu tikhoza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu.

Yesu ndi “choonadi.” Iye ankalankhula komanso kuchita zinthu mogwirizana ndi choonadi. Zinali ngati kuti anthu akaona Yesu, aona choonadi. Anakwaniritsa maulosi ambiri omwe anakhala “‘Inde’ kudzera mwa iye.” (2 Akorinto 1:20; Yohane 1:14) Maulosi amenewa amatithandiza kumvetsa udindo waukulu umene Yesu ali nawo pothandiza kuti zimene Mulungu amafuna zichitike.—Chivumbulutso 19:10.

Komanso Yesu Khristu ndi “moyo.” Chifukwa chakuti Yesu anapereka moyo wake wopanda uchimo komanso magazi ake, anthufe tikhoza kudzapeza “moyo weniweniwo,” womwe ndi “moyo wosatha.” (1 Timoteyo 6:12, 19; Aefeso 1:7; 1 Yohane 1:7) Yesu adzaukitsa anthu mamiliyoni ambiri amene anamwalira kuti nawonso adzakhale ndi chiyembekezo chokhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso.—Yohane 5:28, 29.

Tonsefe tiyenera kumvetsa bwino udindo umene Yesu ali nawo pokwaniritsa chifuniro cha Mulungu. Tikukhulupirira kuti muphunzira zambiri za Yesu, yemwe ndi “njira, choonadi ndi moyo.”

Onaninso

UTHENGA WABWINO WOCHOKERA KWA MULUNGU

Kodi Mulungu Ali ndi Cholinga Chotani Chokhudza Dziko Lapansili?

Baibulo limafotokoza chifukwa chake Mulungu analenga dzikoli, nthawi imene mavuto adzathe, mmene zinthu zidzakhalire padzikoli komanso anthu amene adzakhale m’dziko la paradaiso.