Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo

 MUTU 107

Mfumu Inaitanira Anthu ku Phwando la Ukwati

Mfumu Inaitanira Anthu ku Phwando la Ukwati

MATEYU 22:1-14

  • FANIZO LA PHWANDO LA UKWATI

Yesu atatsala pang’ono kumaliza utumiki wake anapitirizabe kugwiritsa ntchito mafanizo pofuna kuti anthu onse adziwe zimene alembi komanso ansembe aakulu ankachita. Chifukwa cha zimenezi, alembi komanso ansembe aakuluwo ankafuna kumupha. (Luka 20:19) Koma Yesu anafotokozanso fanizo lina. Iye anati:

“Ufumu wakumwamba uli ngati mfumu imene inakonza phwando la ukwati wa mwana wake. Ndipo inatuma akapolo ake kuti akaitane anthu oitanidwa ku phwando laukwati, koma anthuwo sanafune kubwera.” (Mateyu 22:2, 3) Yesu anayamba kufotokoza fanizoli ndi mawu akuti “Ufumu wakumwamba.” Ndiye kuti “mfumu” ya m’fanizoli ndi Yehova Mulungu. Nanga mwana wa mfumuyo komanso anthu amene anaitanidwa ku phwando laukwati ndi ndani? Pamenepanso n’zosavuta kuzindikira kuti mwana wa mfumuyo ndi Mwana wa Yehova, amene ankanena fanizoli ndipo amene anaitanidwawo ndi anthu amene adzalamulire ndi Mwanayo mu Ufumu wakumwamba.

Kodi ndani amene anali oyamba kuitanidwa? Ayenera kuti anali Ayuda chifukwa ndi amene Yesu ndi atumwi ankawalalikira za Ufumu. (Mateyu 10:6, 7; 15:24) Mu 1513 B.C.E., Ayudawo anapanga pangano ndi Mulungu ndipo anavomereza kuti adzatsatira Chilamulo chimene anawapatsa. Choncho Ayuda anali anthu oyambirira kupanga “ufumu wa ansembe.” (Ekisodo 19:5-8) Koma kodi anaitanidwa liti ku “phwando la ukwati?” Anayamba kuitanidwa mu 29 C.E. pamene Yesu anayamba kulalikira za Ufumu wakumwamba.

Kodi Aisiraeli ambiri anatani ataitanidwa? Yesu ananena kuti “anthuwo sanafune kubwera.” Atsogoleri achipembedzo komanso anthu ambiri sanavomereze kuti Yesu anali Mesiya komanso Mfumu yosankhidwa ndi Mulungu.

Koma Yesu anasonyeza kuti Ayudawo adzapatsidwanso mwayi wina. Iye anati: “Kenako inatumanso akapolo ena kuti, ‘Kauzeni oitanidwawo kuti: “Ine ndakonza chakudya chamasana, ng’ombe zanga komanso nyama zanga zonenepa zaphedwa, ndipo zinthu zonse zakonzedwa kale. Bwerani ku phwando laukwati.”’ Koma anthuwo ananyalanyaza ndi kuchoka. Wina anapita kumunda wake, wina kumalonda ake.  Koma enawo anagwira akapolo akewo, ndi kuwachitira zachipongwe n’kuwapha.” (Mateyu 22:4-6) Ndipo zimenezi ndi zimene zinachitika mpingo wachikhristu utangokhazikitsidwa kumene. Nthawi imeneyi, Ayuda anali ndi mwayi wolowa nawo mu Ufumu koma ambiri anakana mwayi umenewu mpaka kufika pozunza ‘akapolo a mfumu.’—Machitidwe 4:13-18; 7:54, 58.

Kodi mtunduwu unakumana ndi zotani chifukwa chochita zimenezi? Yesu ananena kuti: “Pamenepo mfumu ija inakwiya kwambiri, ndipo inatumiza asilikali ake kukawononga opha anthu amenewo ndi kutentha mzinda wawo.” (Mateyu 22:7) Zimenezi zinachitika mu 70 C.E. pamene Aroma anawononga “mzinda [wa Ayuda]” wa Yerusalemu.

Chifukwa chakuti Ayuda anakana mfumu itawaitana, ndiye kuti palibe aliyense amene akanaitanidwa? Ayi. Tikutero chifukwa fanizo la Yesu limapitiriza kuti: “Kenako [mfumu] anauza akapolo ake kuti, ‘Phwando laukwati ndiye lakonzedwa ndithu, koma oitanidwa aja anali osayenera. Chotero pitani m’misewu yotuluka mumzinda, ndipo aliyense amene mukam’peze, mukamuitanire phwando laukwatili.’ Choncho akapolowo anapita m’misewu ndi kusonkhanitsa onse amene anawapeza, oipa ndi abwino omwe. Ndipo chipinda chodyeramo phwando laukwati chinadzaza ndi anthu oyembekezera kulandira chakudya.”—Mateyu 22:8-10.

Izi zinayamba kuchitika pamene mtumwi Petulo anayamba kuthandiza anthu a mitundu ina, omwe sanali Ayuda komanso amene sanatembenukire ku Chiyuda, kuti nawonso akhale Akhristu. Mwachitsanzo mu 36 C.E., Koneliyo, yemwe anali kapitawo wa gulu la asilikali achiroma, ndi anthu a m’banja lake analandira mzimu wa Mulungu. Zimenezi zinawapatsa mwayi wolowa mu Ufumu wakumwamba umene Yesu ananena.—Machitidwe 10:1, 34-48.

Fanizo la Yesu linasonyezanso kuti si onse amene anabwera ku phwandolo omwe “mfumu” inawavomereza. Yesu anati: “Pamene mfumu ija inalowa kukayendera alendowo, inaona munthu wina mmenemo amene sanavale chovala chaukwati. Chotero inamufunsa kuti, ‘Bwanawe! Walowa bwanji muno usanavale chovala cha ukwati?’ Iye anasowa chonena. Kenako mfumuyo inauza atumiki ake kuti, ‘M’mangeni manja ndi miyendo ndipo mum’ponye kunja kumdima. Kumeneko akalira ndi kukukuta mano.’ “Pakuti oitanidwa ndi ambiri, koma osankhidwa ndi owerengeka.”—Mateyu 22:11-14.

N’kutheka kuti atsogoleri achipembedzo amene anamva Yesu akunena zimenezi sanamvetse zimene ankatanthauza. Komabe anthuwa anakwiya kwambiri ndipo anatsimikiza kuti athane ndi Yesu chifukwa ankawachititsa manyazi.

Onaninso

NSANJA YA OLONDA

Yehova “Alibe Tsankho”

Mulungu amamva mapephero a atumiki ake kaya akhale amtundu uti kapena dziko liti, olemera kaya osauka. Kodi timadziwa bwanji zimenezi?