Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo

 MUTU 129

Pilato Ananena Kuti: “Taonani! Mwamuna Uja Ndi Uyu!”

Pilato Ananena Kuti: “Taonani! Mwamuna Uja Ndi Uyu!”

MATEYU 27:15-17, 20-30 MALIKO 15:6-19 LUKA 23:18-25 YOHANE 18:39–19:5

  • PILATO ANAYESA KUMASULA YESU

  • AYUDA ANAPEMPHA KUTI AWAMASULIRE BARABA

  • YESU ANAZUNZIDWA KOMANSO ANAMUCHITIRA ZACHIPONGWE

Pilato anauza anthu amene ankafuna kuti Yesu aphedwe kuti: “Inetu . . . sindinamupeze ndi chifukwa chomuimbira milandu imene mukumunenezayi. Ndipotu ngakhale Herode sanam’peze ndi mlandu.” (Luka 23:14, 15) Chifukwa chakuti Pilato ankafuna kumasula Yesu, anagwiritsa ntchito njira ina. Iye anauza anthuwo kuti: “Muli ndi mwambo wakuti ndizikumasulirani munthu mmodzi pa pasika. Kodi mukufuna ndikumasulireni mfumu ya Ayuda?”—Yohane 18:39.

Pilato ankadziwa munthu wina dzina lake Baraba yemwe anali m’ndende chifukwa chakuti anali wakuba, woukira boma komanso chigawenga. Ndiyeno anafunsa anthuwo kuti: “Kodi mukufuna ndikumasulireni ndani, Baraba kapena Yesu, uja amamuti Khristu?” Anthuwo ananena kuti awamasulire Baraba osati Yesu. Iwo ananena zimenezi chifukwa anachita kuuzidwa ndi ansembe aakulu. Pamenepo Pilato anafunsanso kuti: “Ndani mwa awiriwa amene mukufuna kuti ndikumasulireni?” Gulu la anthulo linafuula kuti: “Baraba.”—Mateyu 27:17, 21.

Pilato atakhumudwa ndi zimene anthuwo anayankha, anawafunsa kuti: “Nanga Yesu, uja amamuti Khristu, ndichite naye chiyani?” Anthuwo anafuula kuti: “Apachikidwe ameneyo!” (Mateyu 27:22) N’zomvetsa chisoni kuti anthuwa ankafuna kuti munthu yemwe anali wosalakwa aphedwe. Ndiyeno Pilato anafunsa kuti: “Chifukwa chiyani? Kodi iyeyu walakwa chiyani? Ine sindikumupeza ndi chifukwa chilichonse chomuphera, choncho ndimukwapula ndi kumumasula.”—Luka 23:22.

Pilato anayesetsa kuti amasule Yesu koma anthu okwiyawo anafuula kuti: “Apachikidwe basi!” (Mateyu 27:23) Atsogoleri achipembedzo ndi amene anasokoneza maganizo a anthuwa n’cholinga choti aphetse Yesu yemwe anali munthu wosalakwa. Ndipotu masiku 5 m’mbuyomo Yesu yemweyu ndi amene analowa mu Yerusalemu ngati Mfumu ndipo anthu anamulandira ndi manja awiri. Ngati ophunzira a Yesu analipo pa nthawi imene anthu ankafuula kuti Yesu apachikidwe, ndiye kuti sanalankhule kalikonse komanso sankafuna kuti anthu awazindikire.

Ndiyeno Pilato anazindikira kuti zimene ankafuna kuchita kuti amasule Yesu sizitheka. Gulu la anthulo litayamba kuchita zachipolowe, Pilato anatenga madzi n’kusamba m’manja anthuwo akuona. Kenako anawauza kuti: “Ndilibe mlandu wa magazi a munthu uyu. Zonse zili kwa inu.” Ngakhale kuti Pilato analankhula zimenezi anthuwo sanasinthe maganizo awo. M’malomwake anamuyankha kuti: “Magazi ake akhala pa ife ndi pa ana athu.”—Mateyu 27:24, 25.

Pofuna kusangalatsa anthuwo, Pilato anachita zinthu zomwe ankadziwa kuti sizoyenera. Anamasula Baraba mogwirizana ndi zomwe anthuwo ankafuna  koma anamuvula Yesu malaya kenako n’kumukwapula.

Asilikali atamaliza kumenya Yesu analowa naye m’nyumba. Gulu la asilikalilo linasonkhananso ndipo linapitiriza kumuchitira zinthu zachipongwe. Asilikaliwo analuka chisoti chachifumu chaminga chomwe anachikanikiza m’mutu mwake. Anapatsanso Yesu bango kuti atenge kudzanja lake lamanja ndipo anamuveka chinsalu chofiira chomwe nthawi zambiri ankavala ndi anthu olemekezeka. Kenako anayamba kumunena monyoza kuti: “Mtendere ukhale nanu, inu Mfumu ya Ayuda!” (Mateyu 27:28, 29) Kuwonjezera pamenepo ankamulavulira komanso kumumenya mbama. Anamulandanso bango lija n’kuyamba kumumenya nalo m’mutu, ndipo zimenezi zinkachititsa kuti minga za “chisoti chachifumu” chija zimubaye kwambiri m’mutu.

Pilato anachita chidwi kwambiri ataona kuti Yesu anali wodekha komanso wolimba mtima pa nthawi yonse imene anthu ankamuchitira zinthu zachipongwe. Choncho pofuna kuti asapezeke wolakwa pa mlanduwu, Pilato anafunanso kumasula Yesu ndipo ananena kuti: “Onani! Ndikumutulutsa panja pano kwa inu, kuti mudziwe kuti sindikupeza mlandu mwa iye.” Mwina Pilato anatulutsa Yesu ali ndi mabala komanso akutuluka magazi n’cholinga choti anthuwo asinthe maganizo awo. Ndiyeno Yesu ataimirira pamaso pa anthu ouma mtimawo, Pilato ananena kuti: “Taonani! Mwamuna uja ndi uyu!”—Yohane 19:4, 5.

Ngakhale kuti Yesu anali atamenyedwa komanso kuvulazidwa anakhalabe wodekha moti ngakhale Pilato analankhula mwaulemu komanso mosonyeza kuti ankamumvera chisoni.