Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 106

Mafanizo Awiri Onena za Munda wa Mpesa

Mafanizo Awiri Onena za Munda wa Mpesa

MATEYU 21:28-46 MALIKO 12:1-12 LUKA 20:9-19

  • FANIZO LONENA ZA ANA AWIRI

  • FANIZO LA ALIMI OSAMALIRA MUNDA WA MPESA

Ali kukachisi Yesu anasokoneza ansembe aakulu ndi akulu amene anamufunsa kuti awauze kumene ankatenga ulamuliro umene ankachitira zinthu. Zimene anawayankha zinawasowetsa chonena. Kenako Yesu ananena fanizo limene linasonyeza kuti ansembe aakulu ndi akuluwo anali anthu otani.

Iye anati: “Munthu wina anali ndi ana awiri. Ndipo anapita kwa mwana woyamba n’kumuuza kuti: ‘Mwana wanga, lero upite kukagwira ntchito m’munda wa mpesa.’ Iye poyankha anati, ‘Ndipita bambo,’ koma sanapite. Kenako anapita kwa mwana wachiwiri uja n’kumuuzanso chimodzimodzi. Iye poyankha anati, ‘Ayi sindipita.’ Koma pambuyo pake anamva chisoni ndipo anapita. Ndani mwa ana awiriwa amene anachita chifuniro cha bambo ake?” (Mateyu 21:28-31) Anthuwa sanavutike kupeza yankho la funsoli. Mwana wachiwiri ndi amene pomaliza anachita zimene bambo ake ankafuna.

Ndiyeno Yesu anauza anthu amene ankamutsutsawo kuti: “Ndithu ndikukuuzani kuti okhometsa msonkho ndi mahule akukusiyani m’mbuyo n’kukalowa mu ufumu wa Mulungu.” Poyamba okhometsa msonkho komanso mahule sankatumikira Mulungu. Koma kenako anthu amenewa analapa ndipo anayamba kutumikira Mulungu. Zimenezi ndi zofanana ndi zimene mwana wachiwiri uja anachita. Koma atsogoleri achipembedzo anali ngati mwana woyamba uja. Iwo ankaoneka ngati ankatumikira Mulungu koma zoona zake n’zoti sankamutumikira. Yesu ananena kuti: “Pakuti Yohane [M’batizi] anabwera kwa inu m’njira yachilungamo, koma inu simunam’khulupirire. Koma okhometsa msonkho ndi mahule anam’khulupirira, Ngakhale kuti inu munaona zimenezi, simunamve chisoni n’kusintha maganizo anu kuti mum’khulupirire.”—Mateyu 21:31, 32.

Yesu atamaliza kunena fanizo limeneli ananenanso fanizo lina. Ananena fanizo lachiwirili pofuna kusonyeza kuti atsogoleri achipembedzo sankafuna kutumikira Mulungu komanso kuti anali anthu oipa. Iye ananena kuti: “Munthu wina analima munda wa mpesa ndi kumanga mpanda kuzungulira mundawo. Komanso anakumba dzenje loponderamo mphesa, ndi kumanga nsanja. Atatero anausiya m’manja mwa alimi n’kupita kudziko lina. Tsopano nyengo ya zipatso itakwana, iye anatumiza kapolo wake kwa alimiwo kuti akam’patseko zina mwa zipatso za m’munda wa mpesawo. Koma iwo anam’gwira, n’kumumenya ndi kum’bweza chimanjamanja. Iye anatumizanso kapolo wina kwa iwo koma ameneyu anamutema m’mutu ndi kumuchitira zachipongwe. Anatumizanso wina, koma ameneyo anamupha. Ndiyeno anatumizanso akapolo ena ambiri. Ena mwa iwo anawamenya ndipo ena anawapha.”—Maliko 12:1-5.

Kodi anthu amene ankamva Yesu akunena fanizo limeneli anamvetsa tanthauzo lake? N’kutheka kuti anthuwo anakumbukira mawu amene Yesaya analemba akuti: “Ine ndine Yehova wa makamu ndipo Isiraeli ndi munda wanga wa mpesa. Amuna a ku Yuda ndiwo mitengo ya mpesa imene ndinali kuikonda. Ine ndinali kuyembekezera chilungamo koma ndinaona anthu akuphwanya malamulo.” (Yesaya 5:7) Anthu komanso zinthu zimene Yesu anatchula m’fanizoli ndi zofanana ndi zimene Yesaya ananena. Tikutero chifukwa mwiniwake wa mundawo ndi Yehova ndipo munda wa mpesa ndi mtundu wa Aisiraeli, womwe unkatetezedwa ndi Chilamulo cha Mulungu. Yehova ankatumiza aneneri kuti azilangiza anthu ake komanso kuwathandiza kuti azibala zipatso zabwino.

Koma ‘alimiwo’ anazunza komanso kupha “akapolo” amene mwinimunda uja anawatuma. Yesu anapitiriza kufotokoza kuti: “Tsopano [mwiniwake wa mundawo] anatsala ndi mmodzi yekha, mwana wake wokondedwa. Anatumizanso mwanayo kwa iwo ngati wotsirizira, n’kunena kuti, ‘Mwana wanga yekhayu akamulemekeza.’ Koma alimiwo anayamba kukambirana kuti, ‘Eya, uyu ndiye wolandira cholowa. Bwerani, tiyeni timuphe, ndipo cholowacho chidzakhala chathu.’ Choncho anamugwira n’kumupha.”—Maliko 12:6-8.

Kenako Yesu anawafunsa anthuwo kuti: “Kodi mwinimunda wa mpesawo adzachita chiyani?” (Maliko 12:9) Atsogoleri achipembedzowo anayankha kuti: “Chifukwa chakuti ndi oipa, adzawawononga koopsa ndipo munda wa mpesawo adzaupereka kwa alimi ena, amene angam’patse zipatso m’nyengo yake.”—Mateyu 21:41.

Ponena mawu amenewa, atsogoleri achipembedzowa anadziweruza okha mosadziwa chifukwa iwo anali  m’gulu la “alimi” ogwira ntchito ‘m’munda wa mpesa’ wa Yehova, womwe unkaimira mtundu wa Isiraeli. Chimodzi mwa zipatso zimene Yehova ankayembekezera kwa alimiwo chinali choti azikhulupirira Mwana wake, yemwenso ndi Mesiya. Yesu anayang’ana atsogoleri achipembedzowo n’kunena kuti: “Kodi simunawerengepo lemba limene limati, ‘Mwala umene omanga nyumba anaukana, umenewu wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri’? Kodi simunawerenge kuti ‘Umenewu wachokera kwa Yehova, ndipo ndi wodabwitsa m’maso mwathu’?” (Maliko 12:10, 11) Kenako Yesu ananena mfundo imene ankafuna kuti anthuwo amvetse. Iye anati: “Ichi n’chifukwa chake ndikukuuzani kuti, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu n’kuperekedwa kwa mtundu wobala zipatso zake.”—Mateyu 21:43.

Alembi komanso ansembe aakulu anazindikira kuti Yesu “anali kunena za iwo mufanizolo.” (Luka 20:19) Pa nthawi imeneyi anthuwo anafunitsitsa kupha Yesu, yemwe anali “wolandira cholowa.” Koma sanamuphe chifukwa ankaopa gulu la anthu, lomwe linkaona kuti Yesu ndi mneneri.