YOHANE 16:1-33

  • YESU ANALI ATATSALA PANG’ONO KUCHOKA NDIPO ATUMWI SAKANAMUONANSO

  • CHISONI CHIMENE ATUMWI ANALI NACHO CHINADZASANDUKA CHISANGALALO

Yesu ndi atumwi ake anakonzeka zotuluka m’chipinda chapamwamba chimene anachitiramo mwambo wa Pasika. Koma asanatuluke Yesu anawapatsanso malangizo ena. Iye anati: “Ndalankhula zimenezi kwa inu kuti musapunthwe.” N’chifukwa chiyani Yesu anawapatsa malangizo amenewa? Iye anawauza kuti: “Anthu adzakuchotsani m’sunagoge. Ndipo nthawi ikubwera pamene aliyense wakupha inu adzaganiza kuti wachita utumiki wopatulika kwa Mulungu.”—Yohane 16:1, 2.

N’kutheka kuti atumwiwo anavutika maganizo kwambiri atamva zimenezi. Ngakhale kuti Yesu anali atawauza kale kuti dziko lidzadana nawo koma anali asanawauzepo kuti adzaphedwa. N’chifukwa chiyani Yesu sanawauze zimenezi? Iye anati: “Zinthu izi sindinakuuzeni pa chiyambi pomwe, chifukwa ndinali pamodzi ndi inu.” (Yohane 16:4) Choncho Yesu anawauza zimenezi asanachoke n’cholinga chowakonzekeretsa maganizo kuti asadzakhumudwe.

Yesu anawauzanso kuti: “Tsopano ndikupita kwa amene anandituma, ndipo palibe aliyense wa inu amene akundifunsa kuti, ‘Mukupita kuti?’” Chakumadzulo tsiku lomwelo, atumwiwo anafunsa Yesu kumene ankapita. (Yohane 13:36; 14:5; 16:5) Koma tsopano atumwiwa atamva kuti adzazunzidwa anachita mantha ndipo anadzimvera chisoni. Chifukwa cha chisonicho analephera kumufunsa za ulemelero umene Yesu ankayembekezera komanso mmene ulemelerowo ukanathandizira anthu amene amalambira Mulungu. Ataona kuti atumwiwo ali ndi chisoni, Yesu ananena kuti: “Chifukwa ndalankhula zimenezi kwa inu, chisoni chadzaza m’mitima yanu.”—Yohane 16:6.

Kenako Yesu ananena kuti: “Ndikupita kuti inu mupindule. Pakuti ngati sindipita, ndiye kuti mthandizi uja sabwera kwa inu. Koma ndikapita, ndikamutumiza kwa inu.” (Yohane 16:7) Kuti ophunzira a Yesu alandire mzimu woyera, pankafunika kuti Yesuyo afe, aukitsidwe kenako apite kumwamba. Ndiyeno ali kumwambako, Yesu akanatumiza mzimu woyera womwe ukanathandiza anthu ake onse padziko lapansi.

Mzimu woyera ‘udzapereka umboni wotsimikizika ku dzikoli wonena za tchimo, za chilungamo, ndi za chiweruzo.’ (Yohane 16:8) Mzimu woyera unapereka umboni wotsimikizira kuti Yesu analidi Mwana wa Mulungu ndiponso kuti anthu sanamukhulupirire. Yesu atakwera kumwamba zinasonyeza kuti anali munthu wolungama komanso zinasonyeza chifukwa chake Satana, amene ndi “wolamulira wa dziko lino,” ayenera kuweruzidwa.—Yohane 16:11.

Yesu ananenanso kuti: “Ndili ndi zambiri zakuti ndikuuzeni, koma padakali pano simungathe kuzimvetsa zonsezo.” Yesu atatumiza mzimu woyera, mzimuwo unathandiza ophunzirawo kuti amvetse “choonadi chonse” moti kuyambira nthawi imeneyo zimene ankachita komanso kulankhula zinali zogwirizana ndi choonadicho.—Yohane 16:12, 13.

Koma kenako atumwiwo anadabwa ndi zimene Yesu ananena. Iye anati: “Kwa kanthawi simudzandionanso, ndipo kwa kanthawi mudzandiona.” Iwo anayamba kufunsana zimene Yesu ankatanthauza. Yesu atazindikira zimenezi anawafotokozera kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Mudzagwetsa misozi ndi kulira mofuula, koma dzikoli lidzasangalala. Mudzamva chisoni, koma chisoni chanu adzachisandutsa chimwemwe.” (Yohane 16:16, 20) Yesu anaphedwa tsiku lotsatira chakumasana. Ataphedwa, atsogoleri achipembedzo anasangalala pomwe ophunzira ake anali ndi chisoni. Koma Yesu ataukitsidwa, ophunzira ake anasiya kumva chisoni n’kuyamba kusangalala ndipo anasangalala kwambiri Yesu atawatumizira mzimu woyera wa Mulungu.

Yesu anayerekezera zimene atumwiwo ankayembekezera kukumana nazo ndi zimene zimachitikira mzimayi amene watsala pang’ono kubereka. Iye ananena kuti: “Pamene mayi akubereka amazunzika kwambiri, chifukwa nthawi yake yafika. Koma mwana akabadwa, sakumbukiranso kupweteka konse kuja chifukwa cha chimwemwe kuti munthu wabadwa padziko.” Koma anawalimbikitsa kuti: “Inunso muli ndi chisoni panopa. Koma ndidzakuonaninso, ndipo mitima yanu idzasangalala. Palibenso amene adzathetse chimwemwe chanu.”—Yohane 16:21, 22.

Pa nthawiyi, atumwi anali asanapempheko chilichonse m’dzina la Yesu. Ndiyeno Yesu anawauza  kuti: “Pa tsikulo mudzapempha m’dzina langa.” Sikuti ankayenera kuchita zimenezi chifukwa chakuti Atate sakanawayankha. Tikutero chifukwa Yesu ananena kuti: “Atateyo amakukondani, chifukwa munandikonda ine . . . monga nthumwi ya Atate.”—Yohane 16:26, 27.

Zimene Yesu anauza atumwiwo zinawalimbikitsa kwambiri moti iwo ananena kuti: “Pa chifukwa chimenechi tikukhulupirira kuti munachokeradi kwa Mulungu.” Koma atumwiwa anali atatsala pang’ono kuyesedwa. Yesu anawauza zimene ankayembekezera kukumana nazo kuti: “Taonani! Nthawi ikubwera, ndipo yafika kale. Mubalalika aliyense kupita kunyumba kwake, ndipo mundisiya ndekha.” Koma anawatsimikizira kuti: “Ndanena zimenezi kwa inu kuti mukhale mu mtendere chifukwa cha ine. M’dzikomu mukumana ndi masautso, koma limbani mtima. Ine ndaligonjetsa dziko.” (Yohane 16:30-33) Pamenepatu sikuti Yesu ankatanthauza kuti angowasiya osawathandiza. Yesu ankadziwa kuti atumwiwo adzagonjetsanso dziko mofanana ndi iyeyo ngati akanapitirizabe kuchita chifuniro cha Mulungu pamene akuyesedwa ndi Satana komanso dzikoli.