MATEYU 26:30, 36-46 MALIKO 14:26, 32-42 LUKA 22:39-46 YOHANE 18:1

  • ZIMENE ZINACHITIKA YESU ATAPITA KUMUNDA WA GETSEMANE

  • THUKUTA LAKE LINAONEKA NGATI MADONTHO A MAGAZI

Yesu atamaliza kupemphera ndi atumwi ake ‘anaimba nyimbo zotamanda Mulungu’ kenako “anatuluka n’kupita kuphiri la Maolivi.” (Maliko 14:26) Iwo analowera chakummawa komwe kunali munda wa Getsemane umene Yesu ankakonda kupitako nthawi zambiri.

Atafika kumundako, komwe kunali mitengo yambiri ya maolivi, Yesu anauza atumwi ake 8 kuti amudikire ndipo iye anatengana ndi atumwi atatu. N’kutheka kuti Yesu anawauza kuti adikirire pamalo olowera m’mundawo chifukwa ananena kuti: “Khalani pansi pompano, ine ndikupita uko kukapemphera.” Yesu anatengana ndi Petulo, Yakobo ndi Yohane ndipo analowa m’mundamo. Iye anavutika kwambiri mumtima ndipo anauza atumwi atatuwo kuti: “Moyo wanga ukumva chisoni chofa nacho. Khalani pompano ndipo mukhalebe maso pamodzi ndi ine.”—Mateyu 26:36-38.

Yesu anawasiyanso atumwi atatu aja n’kuyenda kamtunda pang’ono kenako “anadzigwetsa pansi ndipo anayamba kupemphera.” Kodi Yesu ankapempha chiyani kwa Atate wake pa nthawi yovutayi? Iye anapemphera kuti: “Atate, zinthu zonse n’zotheka kwa inu. Ndichotsereni kapu iyi. Komatu osati mwa kufuna kwanga, koma mwa kufuna kwanu.” (Maliko 14:35, 36) Kodi ankatanthauza chiyani ponena mawu amenewa? Kodi ankafuna kuthawa udindo wopulumutsa anthu? Ayi.

Yesu ali kumwamba ankaona mmene Aroma ankazunzira komanso kuphera anthu. Choncho ankadziwa zimene akumane nazo chifukwa pa nthawiyi anali ndi thupi ngati lathuli ndipo ankamva kupweteka. Koma Yesu ankavutika kwambiri chifukwa ankadziwa kuti aphedwa ngati chigawenga ndipo zimenezi zikanachititsa kuti anthu anyoze dzina la Atate wake. Pa nthawiyi anali atatsala ndi maola ochepa kuti apachikidwe pamtengo ngati mmene zinkakhalira ndi munthu amene wanyoza Mulungu.

Atapemphera kwa kanthawi, Yesu anabwerera kwa atumwi ake atatu aja ndipo anawapeza akugona. Iye anafunsa Petulo kuti: “Zoona anthu inu simungathe kukhalabe maso limodzi ndi ine ola limodzi? Khalani maso ndipo pempherani kosalekeza kuti musalowe m’mayesero.” Yesu ankadziwa kuti atumwi ake atopa kwambiri komanso kunali kutada. N’chifukwa chake ananena kuti: “Zoona, mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.”—Mateyu 26:40, 41.

Kenako Yesu anapitanso kukapemphera kachiwiri ndipo anapempha Mulungu kuti amuchotsere “kapu iyi.” Atabwerako anapezanso atumwi atatuwo akugona ngakhale kuti pa nthawiyi ankafunika kuti akhale akupemphera kuti asalowe m’mayesero. Yesu atawafunsa chifukwa chake ankagonanso “anasowa chomuyankha.” (Maliko 14:40) Yesu anapitanso kachitatu ndipo anagwada n’kuyamba kupemphera.

Yesu ankada nkhawa kwambiri kuti akaphedwa ngati chigawenga zichititsa kuti anthu anyoze dzina la Atate wake. Yehova anamva zimene Mwana wake ankamupempha moti anamutumizira mngelo kuti amulimbikitse. Komabe Yesu sanasiye kuchonderera Atate wake ndipo anapitiriza “kupemphera ndi mtima wonse.” Pa nthawiyi Yesu anavutika maganizo kwambiri chifukwa chodziwa udindo waukulu womwe anali nawo. Ngati akanalephera kupilira akanataya  mwayi wodzakhala ndi moyo mpaka kalekale komanso anthu amene ankamukhulupirira sakanakhala ndi chiyembekezo chodzapeza moyo wosatha. Yesu anavutika kwambiri moti “thukuta lake linaoneka ngati madontho amagazi amene akugwera pansi.”—Luka 22:44.

Yesu atabwerera kachitatu anapezanso ophunzira ake akugona. Iye ananena kuti: “Zoona nthawi ngati ino mukugona ndi kupumula! Taonani! Ola lakuti Mwana wa munthu aperekedwe m’manja mwa ochimwa layandikira. Nyamukani, tiyeni tizipita. Onani! Wondipereka uja ali pafupi.”—Mateyu 26:45, 46.