Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo

 MUTU 137

Anaonekera kwa Anthu Ambiri Mwambo wa Pentekosite Usanachitike

Anaonekera kwa Anthu Ambiri Mwambo wa Pentekosite Usanachitike

MATEYU 28:16-20 LUKA 24:50-52 MACHITIDWE 1:1-12; 2:1-4

  • YESU ANAONEKERA KWA ANTHU AMBIRI

  • YESU ANAKWERA KUMWAMBA

  • YESU ANATUMIZA MZIMU WOYERA KWA OPHUNZIRA 120

Yesu ataukitsidwa anakonza zoti akakumane ndi atumwi ake 11 paphiri lina ku Galileya. Ophunzira enanso pafupifupi 500 anafikanso pamalowa ndipo ena mwa iwo ankakayikirabe kuti Yesu waukitsidwa. (Mateyu 28:17; 1 Akorinto 15:6) Koma zimene Yesu anawauza pa nthawiyi zinathandiza aliyense kuti akhulupiriredi zoti iye anauka.

Yesu anawauza kuti Mulungu anamupatsa mphamvu zolamulira kumwamba komanso padziko lapansi. Iye analimbikitsa ophunzira ake kuti: “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera, ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.” (Mateyu 28:18-20) N’zosangalatsa kuti Yesu ataukitsidwa ankafunitsitsa kuti uthenga wabwino ulalikidwe.

Otsatira onse a Yesu amene analipo pa nthawi imeneyo, kaya ndi amuna, akazi komanso ana, anapatsidwa ntchito yophunzitsa anthu kuti akhale ophunzira ake. Anawauzanso kuti anthu otsutsa adzayesetsa kulepheretsa ntchito yolalikira komanso yophunzitsa anthu ndipo anawalimbikitsa kuti: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.” Kodi zimenezi zinawalimbikitsa bwanji otsatira akewo? Yesu anawauza kuti: “Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” Yesu sankatanthauza kuti anthu onse amene adzagwire nawo ntchito yolalikira adzapatsidwa mphamvu zochitira zozizwitsa. Koma ankatanthauza kuti mzimu woyera udzawathandiza kugwira ntchitoyi.

Yesu atangoukitsidwa anaonekera kwa ophunzira ake kwa “masiku onse 40.” Pa nthawi imeneyo iye ankaonekera kwa ophunzira ake ali ndi thupi ngati lathuli pofuna kuwapatsa ‘umboni wotsimikizika, . . . kuti ali moyo.’ Anawapatsanso malangizo onena “za ufumu wa Mulungu.”—Machitidwe 1:3; 1 Akorinto 15:7.

Zikuoneka kuti atumwiwo ali ku Galileya, Yesu anawauza kuti abwerere ku Yerusalemu. Atakumana nawo ku Yerusalemuko anawauza kuti: “Musatuluke mu Yerusalemu, koma muyembekezere chimene Atate analonjeza, chimene munamva kwa ine. Chifukwa Yohane anabatizadi ndi madzi, koma pasanathe masiku ambiri mudzabatizidwa ndi mzimu woyera.”—Machitidwe 1:4, 5.

Kenako Yesu anakumananso ndi atumwi ake ndipo “anawatsogolera kupita nawo ku Betaniya.” Betaniya anali chakum’mawa, kumunsi kwa phiri la Maolivi. (Luka 24:50) Ngakhale kuti Yesu anali atawauza zoti apita kumwamba, atumwiwo ankaganizabe kuti Ufumu wake ukhazikitsidwa padziko lapansi pa nthawiyo.—Luka 22:16, 18, 30; Yohane 14:2, 3.

Moti anamufunsa Yesu kuti: “Ambuye, kodi mubwezeretsa ufumu kwa Isiraeli pa nthawi ino?” Koma iye anangowayankha kuti: “Si kwa inu kudziwa nthawi kapena nyengo zimene Atate waziika pansi pa ulamuliro wake.” Kenako anawauzanso za ntchito imene ankafunika kugwira. Iye anati: “Mzimu woyera ukadzafika pa inu, mudzalandira mphamvu. Pamenepo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”—Machitidwe 1:6-8.

Yesu adakali pamodzi ndi atumwi ake aja paphiri la Maolivi, anayamba kukwera kumwamba. Kenako mtambo unamuphimba moti atumwi ake aja sanamuonenso. Yesu ataukitsidwa ankaonekera kwa anthu ali ndi thupi ngati lathuli. Koma pa nthawiyi, Yesu anakwera kumwamba ali ndi thupi lauzimu. (1 Akorinto 15:44, 50; 1 Petulo 3:18) Atumwi okhulupirikawo ankangoyang’anitsitsabe Yesu akukwera kumwamba koma kenako anaona “amuna awiri ovala zoyera” ataima pambali pawo. Amunawo anali angelo ndipo anawafunsa kuti: “Amuna inu a ku Galileya, n’chifukwa chiyani muli chilili choncho kuyang’ana kuthambo? Yesu ameneyu, amene watengedwa kupita kumwamba kuchoka pakati panu, adzabwera m’njira yofanana ndi mmene mwamuonera akukwera kuthambo.”—Machitidwe 1:10, 11.

Pamene Yesu ankachoka padziko lapansi kupita kumwamba, ndi otsatira ake okhulupirika okha omwe anamuona. Choncho “adzabwera m’njira yofanana” kutanthauza kuti ndi otsatira ake okhulupirika okha  amene adzazindikire kuti Yesu wayamba kulamulira monga Mfumu.

Zimenezi zitachitika, atumwi anabwerera ku Yerusalemu. Atafika atumwiwo limodzi ndi ophunzira ena, kuphatikizapo “Mariya mayi a Yesu, . . . ndi abale ake a Yesu” anayamba kusonkhana. (Machitidwe 1:14) Anthuwa ankati akasonkhana ankapemphera. Nkhani imodzi imene anaipempherera kwambiri inali yosankha wophunzira wina woti alowe m’malo mwa Yudasi Isikarioti kuti nambala ya atumwi ikhalebe 12. (Mateyu 19:28) Ankafuna kusankha wophunzira amene anaona zimene Yesu anachita ali padziko lapansi komanso amene anamuona ataukitsidwa. Posankha wophunzirayo anachita maere kuti asankhe zinthu mogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna. Aka kanali komaliza kuti maere atchulidwe m’Baibulo. (Salimo 109:8; Miyambo 16:33) Anasankha Matiya, yemwe mwina anali m’gulu la ophunzira 70 amene Yesu anawatuma kuti akalalikire ndipo “anamuphatikiza pa atumwi 11 aja.”—Machitidwe 1:26.

Patangotha masiku 10, Yesu atapita kumwamba, Ayuda anachita mwambo wa Pentekosite wa mu 33 C.E. Pa tsikuli ophunzira pafupifupi 120 anasonkhana m’chipinda china chapamwamba ku Yerusalemu. Mwadzidzidzi m’chipindamo munamveka phokoso la mphepo yamphamvu. Ndiyeno panaoneka malawi a moto ooneka ngati malilime ndipo malawiwo anali pamutu pa wophunzira aliyense. Kenako ophunzira onsewo anayamba kulankhula zinenero zosiyanasiyana. Umenewu unali umboni wakuti ophunzirawo alandira mzimu woyera umene Yesu analonjeza kuti adzawatumizira.—Yohane 14:26.