MACHITIDWE 7:56

  • YESU ANAKHALA KUDZANJA LAMANJA LA MULUNGU

  • SAULO ANAKHALA WOPHUNZIRA

  • TILI NDI CHIFUKWA CHOKHALIRA OSANGALALA

Patapita masiku 10 Yesu atakwera kumwamba, ophunzira ake analandira mzimu woyera pa tsiku la mwambo wa Pentekosite. Umenewu unali umboni wakuti Yesu ali kumwamba. Kenako panachitikanso zinthu zina zomwe zinatsimikiziradi kuti Yesu ali kumwamba. Sitefano, yemwe anali wophunzira wa Yesu, atatsala pang’ono kuponyedwa miyala chifukwa cholalikira mokhulupirika ananena kuti: “Taonani! Ndikuona kumwamba kotseguka, ndipo Mwana wa munthu waimirira kudzanja lamanja la Mulungu.”—Machitidwe 7:56.

Yesu atafika kumwamba anadikirira kuti Atate wake amuuze zoyenera kuchita, zomwe zinalembedwa kalekale m’Mawu a Mulungu. Mulungu anauza Davide kulemba kuti: “Yehova wauza Ambuye wanga [Yesu] kuti: ‘Khala kudzanja langa lamanja kufikira nditaika adani ako monga chopondapo mapazi ako.’” Nthawi yodikirirayo itatha, Yesu ‘anapita kukagonjetsa anthu pakati pa adani [ake].’ (Salimo 110:1, 2) Koma kodi Yesu ali kumwamba ankachita chiyani podikirira kuti agonjetse adani ake?

Pa mwambo wa Pentekosite wa mu 33 C.E., mpingo wachikhristu unakhazikitsidwa. Kuchokera pa nthawiyi, Yesu ali kumwamba anayamba kulamulira ophunzira ake odzozedwa ndi mzimu woyera. (Akolose 1:13) Ankawatsogolera pa ntchito yolalikira komanso anawakonzekeretsa ntchito yomwe ankayenera kudzagwira m’tsogolo. Kodi ankayenera kudzagwira ntchito yanji? Odzozedwa omwe adzakhale okhulupirika mpaka imfa yawo adzaukitsidwa ndipo adzalamulira ngati mafumu pamodzi ndi Yesu mu Ufumu wake.

Munthu mmodzi amene anadziwika kuti adzalamulira nawo monga mfumu ndi Saulo, yemwe amadziwika ndi dzina lachiroma lakuti Paulo. Saulo anali Myuda, yemwe kwa nthawi yaitali anali wodzipereka potsatira Chilamulo cha Mulungu. Koma atsogoleri achipembedzo achiyuda anasocheretsa Saulo moti anavomereza zoti Sitefano aponyedwe miyala. Zimenezi zitachitika, Saulo anapitiriza “kuopseza ophunzira a Ambuye komanso anali wofunitsitsa kuwapha” moti anayamba ulendo wopita ku Damasiko. Mkulu wa Ansembe Kayafa anapatsa Saulo chilolezo choti akamange ophunzira a Yesu n’kubwera nawo ku Yerusalemu. (Machitidwe 7:58; 9:1) Koma ali m’njira kuwala kothobwa m’maso kunamuzungulira ndipo anagwa pansi.

Kenako Saulo anamva mawu omwe sankadziwa komwe ankachokera akuti: “Saulo, Saulo n’chifukwa chiyani ukundizunza?” Saulo anafunsa kuti: “Mbuyanga, ndinu ndani kodi?” Yankho lake linali lakuti:  “Ndine Yesu, amene iwe ukumuzunza.”—Machitidwe 9:4, 5.

Yesu anauza Saulo kuti alowe mumzinda wa Damasiko ndipo akadikire kuti amupatse malangizo ena. Koma kuti alowe mumzindawo munthu wina anachita kumugwira dzanja n’kumulondolera njira chifukwa kuwala kuja kunamuchititsa kuti asathenso kuona. Ndiyeno Yesu anaonekeranso kwa Hananiya m’masomphenya. Hananiya anali wophunzira wa Yesu amene ankakhala ku Damasiko. Yesu anauza Hananiya mmene angayendere kuti akapeze Saulo. Hananiya sankafuna kukakumana ndi Saulo chifukwa ankachita mantha koma Yesu anamuuza kuti: “Munthu ameneyu ndi chiwiya changa chochita kusankhidwa chotengera dzina langa kupita nalo kwa anthu a mitundu ina, komanso kwa mafumu ndi ana a Isiraeli.” Saulo anayambanso kuona ndipo ali ku Damasiko komweko “anayamba kulalikira za Yesu . . . , kuti Ameneyu ndiye Mwana wa Mulungu.”—Machitidwe 9:15, 20.

Yesu anathandiza Paulo komanso anthu ena kupitirizabe kugwira ntchito yolalikira yomwe anaiyambitsa ali padziko lapansi. Mulungu anawadalitsa ndipo ntchitoyi inayenda bwino kwambiri. Patapita zaka 25 kuchokera pamene Yesu anaonekera kwa Paulo akupita ku Damasiko, Paulo analemba kuti uthenga wabwino ‘walalikidwa m’chilengedwe chonse cha pansi pa thambo.’—Akolose 1:23.

Patapita zaka zambiri Yesu anaonetsa mtumwi Yohane yemwe ankamukonda, masomphenya osiyanasiyana. Masomphenyawo amapezeka m’Baibulo m’buku la Chivumbulutso. Poona masomphenyawa zinali ngati kuti Yohane akuona Yesu atayamba kulamulira ngati Mfumu. (Yohane 21:22) ‘Mwa mzimu, [Yohane] anapezeka kuti ali m’tsiku la Ambuye.’ (Chivumbulutso 1:10) Kodi tsiku limeneli linayamba liti?

Kumvetsa bwino maulosi a m’Baibulo kwatithandiza kudziwa kuti “tsiku la Ambuye,” linayamba m’nthawi yathu ino. M’chaka cha 1914, nkhondo yoyamba yapadziko lonse inayamba. Kungoyambira chaka chimenecho padzikoli panayamba kuchitika nkhondo zambiri, miliri, njala, zivomezi komanso zinthu zina zomwe zikusonyeza kuti “chizindikiro” cha “kukhalapo” komanso “cha mapeto” chimene Yesu anauza atumwi ake chikukwaniritsidwa. (Mateyu 24:3, 7, 8, 14) Tsopano uthenga wabwino wa Ufumu ukulalikidwa m’madera omwe ankalamuliridwa ndi Aroma komanso padziko lonse.

Mulungu anauza Yohane kuti alembe tanthauzo la zimenezi. Analemba kuti: “Tsopano chipulumutso, mphamvu, ufumu wa Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Khristu wake zafika.” (Chivumbulutso 12:10) Ufumu wa Mulungu umene Yesu ankalalikira kwambiri uli kumwamba ndipo ndi weniweni.

Imeneyi ndi nkhani yosangalatsa kwambiri kwa ophunzira onse okhulupirika a Yesu moti amavomereza mawu amene Yohane analemba akuti: “Pa chifukwa chimenechi, kondwerani kumwamba inu ndi inu okhala kumeneko! Tsoka dziko lapansi ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, ndipo ali ndi mkwiyo waukulu podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.”—Chivumbulutso 12:12.

Panopa sikuti Yesu ali kudzanja lamanja la Atate wake n’kumangokhala. Iye akulamulira monga Mfumu ndipo posachedwapa awononga adani ake onse. (Aheberi 10:12, 13) Adani ake akadzawonongedwa moyo udzakhala wosangalatsa kwambiri padziko lapansi.