Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo

 MUTU 113

Fanizo la Matalente Limatiphunzitsa Kufunika Kochita Zinthu Mwakhama

Fanizo la Matalente Limatiphunzitsa Kufunika Kochita Zinthu Mwakhama

MATEYU 25:14-30

  • YESU ANANENA FANIZO LA MATALENTE

Yesu ananenanso fanizo lina pa nthawi imene anali ndi ophunzira ake 4 pa phiri la Maolivi paja. Masiku angapo m’mbuyomo pamene Yesu anali ku Yeriko, ananena fanizo la ndalama za mina pofuna kusonyeza kuti padzadutsa nthawi yaitali Ufumu usanabwere. Fanizo limene ananena pa nthawi imeneyi limanena zinthu zina zofanana ndi zimene ananena m’fanizo la ndalama za mina. Fanizoli limafotokozanso zinthu zina pa nkhani ya kukhalapo kwake komanso zimene zidzachitike dziko la Satanali likadzatsala pang’ono kutha. Limasonyezanso kuti ophunzira ake ayenera kuchita khama pamene akugwiritsa ntchito zinthu zimene apatsidwa.

Yesu ananena kuti: “Zili ngati munthu amene anali kupita kudziko lina, ndipo anaitanitsa akapolo ake ndi kuwasungitsa chuma chake.” (Mateyu 25:14) Atumwi anazindikira mwamsanga kuti “munthu” amene Yesu ankanena m’fanizoli anali iyeyo. Tikutero chifukwa m’mbuyomo Yesu anali atadziyerekezerapo ndi munthu amene anapita ku dziko lakutali “kuti akalandire ufumu.”—Luka 19:12.

Munthu wa m’fanizoli asanapite kudziko lakutali, anapereka chuma chake chamtengo wapatali kwa akapolo kapena kuti antchito ake. Pa zaka zitatu ndi hafu zimene Yesu anachita utumiki wake ankalalikira kwambiri za uthenga wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu ndipo anaphunzitsanso ophunzira ake kuti azigwira ntchitoyi. Tsopano anali atatsala pang’ono kuchoka ndipo ankadziwa kuti ophunzira ake adzapitiriza kugwira ntchito imene anawaphunzitsa.—Mateyu 10:7; Luka 10:1, 8, 9; yerekezerani ndi Yohane 4:38; 14:12.

Kodi munthu wa m’fanizoli anagawa bwanji “chuma chake”? Yesu ananena kuti: “Woyamba anam’patsa ndalama zokwana matalente asanu, wachiwiri anam’patsa matalente awiri, ndipo wachitatu anam’patsa talente imodzi. Aliyense anam’patsa malinga ndi luso lake, ndipo iye anapita kudziko lina.” (Mateyu 25:15) Kodi antchitowa anachita chiyani ndi chuma chimene anapatsidwachi? Kodi anachita zinthu mwakhama pofuna kuthandiza Mbuye wawoyo? Yesu anauza atumwiwo kuti:

“Nthawi yomweyo amene analandira matalente asanu uja ananyamuka kukachita nawo malonda ndipo anapindula matalente enanso asanu. Chimodzimodzinso amene analandira matalente awiri uja, anapindula enanso awiri. Koma amene analandira imodzi yokha uja anapita kukakumba pansi n’kubisa ndalama yasiliva ya mbuye wakeyo.” (Mateyu 25:16-18) Kodi chinachitika n’chiyani Mbuye wawo atabwera?

Yesu ananena kuti: “Patapita nthawi yaitali, mbuye wa akapolowo anabwera ndi kuwerengerana nawo ndalama.” (Mateyu 25:19) Antchito awiri oyambirira anachita zonse zomwe akanatha aliyense “malinga ndi luso lake.” Wantchito aliyense anachita zinthu mwakhama ndipo anapindula pa ndalama zimene anapatsidwa zija. Amene analandira matalente 5, anapezanso matalente ena 5 ndipo amene anapatsidwa matalente awiri, anapezanso ena awiri. (Nthawi imeneyo munthu ankafunika kugwira ntchito zaka pafupifupi 19 kuti apeze ndalama zokwana talente imodzi.) Mbuye uja anayamikira wantchito aliyense kuti: “Wachita bwino kwambiri, kapolo wabwino ndi wokhulupirika iwe! Unakhulupirika pa zinthu zochepa.  Ndikuika kuti uziyang’anira zinthu zambiri. Sangalala limodzi ndi ine mbuye wako.”—Mateyu 25:21.

Koma izi si zimene zinachitikira wantchito amene analandira talente imodzi uja. Wantchito ameneyu ananena kuti: “Ambuye, ndinadziwa kuti inu ndinu munthu wovuta. Mumakolola kumene simunafese, ndipo mumatuta tirigu kumene simunapete. Choncho ndinachita mantha ndipo ndinapita kukabisa talente yanu ija pansi. Nayi ndalama yanu, landirani.” (Mateyu 25:24, 25) Iye sanaganize n’komwe zosungitsa ndalamayo kwa osunga ndalama kuti Mbuye wake adzapeze phindu. Choncho zimene wantchitoyu anachita zinali zosathandiza kwa mbuye wake.

Moti zinali zomveka kuti Mbuyeyo anatchula munthu ameneyu kuti: “Kapolo woipa ndi waulesi iwe.” Iye analandidwanso zinthu zimene anali nazo ndipo anazipereka kwa wantchito wina amene akanagwira ntchito mwakhama. Kenako Mbuyeyo ananena mfundo imene amayendera. Iye anati: “Pakuti amene ali nazo, adzawonjezeredwa zambiri ndipo adzakhala nazo zambiri, koma amene alibe adzalandidwa ngakhalenso zimene ali nazo.”—Mateyu 25:26, 29.

Ophunzira a Yesu anali ndi zinthu zambiri zoti aziganizire ndipo fanizoli linawachititsanso kuti aganizire zinthu zina. Iwo anadziwa kuti Yesu anawapatsa mwayi waukulu kwambiri wothandiza anthu ena kuti akhale ophunzira ake. Yesu ankayembekezera kuti ophunzirawo adzagwira ntchitoyi mwakhama. Koma sankayembekezera kuti ophunzira ake onse adzachita zofanana pogwira ntchito yolalikira imene anawapatsa. Mogwirizana ndi zimene ananena m’fanizo lija aliyense ayenera kuchita zinthu “malinga ndi luso lake.” Choncho zimene zinachitikira wantchito womalizayu zikusonyezeratu kuti Yesu sangasangalale ndi munthu “waulesi” komanso amene akulephera kuchita zonse zomwe angathe pofuna kupindulitsa Mbuye wake.

Atumwiwo ayenera kuti anasangalala kwambiri ndi zimene Yesu anawalonjeza. Iye anati: “Amene ali nazo, adzawonjezeredwa zambiri.”

Onaninso

MAFUNSO OFUNSIDWA KAWIRIKAWIRI

N’chifukwa Chiyani Mumalalikira Kunyumba ndi Nyumba?

Dziwani zimene Yesu anauza ophunzira ake oyambirira kuti azichita.

NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA)

Kodi Tikuphunzira Chiyani pa Fanizo la Matalente?

Nkhaniyi ikusintha zinthu zina zimene tinkazikhulupirira pa fanizo la matalente.