Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo

 MUTU 118

Anakangananso Kuti Wamkulu Ndani

Anakangananso Kuti Wamkulu Ndani

MATEYU 26:31-35 MALIKO 14:27-31 LUKA 22:24-38 YOHANE 13:31-38

  • YESU ANAPEREKA MALANGIZO PA NKHANI YOFUNA UDINDO WAPAMWAMBA

  • YESU ANANENERATU KUTI PETULO AMUKANA

  • OTSATIRA A YESU AMADZIWIKA NDI CHIKONDI

Usiku wake womaliza Yesu anaphunzitsa atumwi ake khalidwe la kudzichepetsa powasambitsa mapazi. N’chifukwa chiyani zinali zoyenera kuti Yesu awaphunzitse khalidwe limeneli? Chifukwa chakuti atumwiwa ankavutika kusonyeza khalidweli. Iwo ankatumikira Mulungu ndi mtima wonse koma ankavutikabe ndi nkhani yakuti wamkulu ndani pakati pawo. (Maliko 9:33, 34; 10:35-37) Zimenezi zinaonekeranso usiku womwewu.

Zimene zinachitika n’zakuti “panabuka mkangano woopsa pakati [pa atumwiwo] za amene anali kuoneka wamkulu kwambiri.” (Luka 22:24) Yesu ayenera kuti anamva chisoni kwambiri ataona kuti atumwiwo akukangananso chifukwa cha nkhani imeneyi. Kodi Yesu anatani?

M’malo mokalipira atumwi akewo chifukwa cha zimene anachitazo komanso chifukwa cha maganizo awo olakwikawo, Yesu analeza mtima n’kuwauza kuti: “Mafumu a mitundu ya anthu amachita ulamuliro pa anthu awo, ndipo amene ali ndi mphamvu pa anthuwo amatchedwa Opereka zabwino. Inu musakhale otero. . . . Kodi wamkulu ndani, amene akudya patebulo kapena amene akutumikira?” Kenako anawakumbutsa chitsanzo chabwino chimene ankawasonyeza nthawi zonse powauza kuti: “Koma ine ndili pakati panu monga wotumikira.”—Luka 22:25-27.

Ngakhale kuti atumwiwa ankalakwitsa zina ndi zina, anasonyeza kuti anali okhulupirika chifukwa anapitirizabe kuyenda ndi Yesu pa nthawi imene ankakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Chifukwa chakuti atumwiwo anali okhulupirika, Yesu ananena kuti: “Ndikuchita nanu pangano, mmene Atate wanga wachitira pangano la ufumu ndi ine.” (Luka 22:29) Atumwiwa anasonyeza kuti anali otsatira a Yesu okhulupirika moti Yesu anawauza kuti adzalamulira naye mu Ufumu wake chifukwa cha pangano limene anapangana nawo.

Ngakhale kuti atumwi anali ndi mwayi wokalamulira ndi Yesu, pa nthawiyi anali adakali ochimwa ndipo ankalakwitsa zina ndi zina. Yesu anawauza kuti: “Satana akufuna anthu inu, kuti akupeteni ngati tirigu,” amene amauluzika akamapetedwa. (Luka 22:31) Anawachenjezanso kuti: “Nonsenu muthawa ndi kundisiya ndekha usiku uno, pakuti Malemba amati, ‘Ndidzapha m’busa, ndipo nkhosa za m’gululo zidzabalalika.’”—Mateyu 26:31; Zekariya 13:7.

Koma Petulo ananena motsimikiza kuti: “Ngakhale ena onse atathawa kukusiyani, ine ndekha sindingathawe!” (Mateyu 26:33) Yesu anauza Petulo kuti usiku umenewo tambala asanalire kawiri amukana. Ndiyeno Yesu ananenanso kuti: “Ine ndakupempherera iwe kuti chikhulupiriro chako chisathe. Chotero iwenso, ukabwerera, ukalimbikitse abale ako.” (Luka 22:32) Komabe Petulo ananenetsa kuti: “Ngati kuli kufa, ine ndifa nanu limodzi, sindingakukaneni.” (Mateyu 26:35) Atumwi enawo ananenanso chimodzimodzi.

Ndiyeno Yesu anauza ophunzira akewo kuti: “Ndikhala nanu kanthawi kochepa chabe. Mudzandifunafuna, ndipo monga ndinauzira Ayuda aja kuti, ‘Kumene ine ndikupita simungathe kukafikako,’ tsopano ndikuuzanso inuyo. Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana. Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.”—Yohane 13:33-35.

Yesu atangonena kuti akhala nawo kanthawi kochepa chabe, Petulo anafunsa kuti: “Ambuye, mukupita kuti?” Pomuyankha anamuuza kuti: “Kumene ndikupita sunganditsatire padakali pano, koma udzanditsatira m’tsogolo.” Petulo anadabwa kwambiri ndipo ananena kuti: “Ambuye, n’chifukwa chiyani sindingakutsatireni padakali pano? Ndidzapereka moyo wanga chifukwa cha inu.”—Yohane 13:36, 37.

Kenako Yesu anakumbutsa atumwiwo za nthawi imene anawatuma kuti akalalikire ku Galileya. Pa nthawi imeneyo anawauza kuti asatenge thumba la ndalama kapena chakudya. (Mateyu 10:5, 9, 10) Ndiyeno anawafunsa kuti: “Munasowa kanthu kodi?” Iwo anayankha kuti: “Ayi.” Koma kodi tsopano anayenera kuchita chiyani? Yesu anawauza kuti: “Amene ali ndi chikwama cha ndalama achitenge, chimodzimodzinso thumba la chakudya. Ndipo amene alibe lupanga  agulitse malaya ake akunja n’kugula lupanga. Pakuti ndikukuuzani kuti mawu olembedwawa ayenera kukwaniritsidwa mwa ine. Mawuwo ndi akuti, ‘Ndipo anamutenga ngati mmodzi wa anthu osamvera malamulo.’ Pakuti chimene chikukhudza ine chikukwaniritsidwa.”—Luka 22:35-37.

Ponena mawu amenewa Yesu ankatanthauza kuti apachikidwa pamtengo pamodzi ndi anthu ochita zoipa ndiponso kuti kenako ophunzira ake adzazunzidwa kwambiri. Ophunzirawo ankaona kuti anali okonzeka moti ananena kuti: “Ambuye, onani! Tili ndi malupanga awiri awa.” Iye anawauza kuti: “Amenewa ndi okwanira.” (Luka 22:38) Chifukwa chakuti ophunzirawo anayankha kuti anali ndi malupanga awiri, Yesu anapezerapo mwayi wowaphunzitsa mfundo ina yofunika kwambiri.