MATEYU 24:3-51 MALIKO 13:3-37 LUKA 21:7-38

  • OPHUNZIRA 4 ANAPEMPHA CHIZINDIKIRO

  • MAULOSI ANAYAMBA KUKWANIRITSIDWA M’NTHAWI YA ATUMWI

  • TIYENERA KUKHALA TCHERU

Lachiwiri masana pa Nisani 11, Yesu ndi ophunzira ake 4 anali atakhala pansi m’phiri la Maolivi. Mayina a ophunzirawa anali Petulo, Andireya, Yakobo ndi Yohane. Yesu anali atatsala pang’ono kumaliza utumiki wake wa padziko lapansi womwe anaugwira mwakhama kwambiri. Iye ankaphunzitsa anthu kukachisi masana ndipo usiku ankakagona kunja kwa mzinda. Anthu ankamvetsera mwachidwi zimene Yesu ankaphunzitsa ndipo ‘ankalawirira m’mawa kwambiri kupita kwa iye kukachisi kuti akamumvetsere.’—Luka 21:37, 38.

Ophunzira 4 aja anapita kwa Yesu ali payekha. Iwo ankada nkhawa chifukwa Yesu anali atangowauza kumene zimene zidzachitikire kachisi kuti sipadzakhala mwala pa mwala unzake. Ophunzirawa ankaganizira zinthu zambiri. Nthawi ina m’mbuyomu Yesu anawauza kuti: “Khalani okonzeka, chifukwa pa ola limene simukuliganizira, Mwana wa munthu adzafika.” (Luka 12:40) Anawauzanso za “tsikulo, pamene Mwana wa munthu adzaonekera.” (Luka 17:30) Kodi zimene anawauzazi zinali zogwirizana ndi nkhani yomwe anali atangowauza yokhudza zimene zidzachitikire kachisi? Ophunzirawo ankafunitsitsa kudziwa zambiri moti anafunsa Yesu kuti: “Tiuzeni, Kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a nthawi ino chidzakhala chiyani?”—Mateyu 24:3.

Zikuoneka kuti ophunzirawa ankaganizira za kuonongedwa kwa kachisi amene ankamuona pamene anali paphiripo. Anafunsanso za kuonekera kwa Mwana wa munthu. Ayenera kuti anakumbukiranso fanizo la Yesu lonena za “munthu wina wa m’banja lachifumu” amene “anapita kudziko lakutali kuti akalandire ufumu ndi kubwerako.” (Luka 19:11, 12) Ophunzirawa ankafunanso kudziwa zinthu zina zimene zidzachitike ku “mapeto a nthawi ino.”

Poyankha ophunzirawa, Yesu anawauza chizindikiro chimene chidzawathandize kudziwa mapeto a nthawi imene ulamuliro wa Ayuda komanso kachisi zidzawonongedwe. Koma Yesu ananenanso kuti chizindikirochi chidzathandizanso Akhristu ena m’tsogolo kudziwa kuti ayamba kukhala m’nthawi ya “kukhalapo” kwake komanso kudziwa kuti mapeto a nthawi ya pansi pano atsala pang’ono kufika.

Pamene zaka zinkadutsa, atumwi anaona kuti zimene Yesu ananena zikuchitikadi. Ndipotu zinthu zambiri zimene Yesu ananena zinayamba kuchitika m’nthawi yawo. Choncho Ayuda amene anakhala tcheru sanadabwe ndi zimene zinachitika mu 70 C.E. M’chakachi ulamuliro wa Ayuda komanso kachisi zinawonongedwa mogwirizana ndi zimene Yesu ananena zaka 37 m’mbuyomo. Komabe si zinthu zonse zimene Yesu ananena zomwe zinachitika pofika mu 70 C.E. Ndiye kodi n’chiyani chomwe chidzakhale chizindikiro cha kukhalapo kwa Yesu monga wolamulira mu Ufumu? Yesu anafotokozera atumwiwo zimene zidzachitike.

Iye ananeneratu kuti mudzamva za “nkhondo ndi mbiri za nkhondo” komanso kuti “mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina.” (Mateyu 24:6, 7) Anawauzanso kuti: “Kudzachitika zivomezi zamphamvu, ndipo kudzakhala miliri ndi njala m’malo osiyanasiyana.” (Luka 21:11) Komanso Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti: “Anthu adzakugwirani ndi kukuzunzani.” (Luka 21:12) Padzakhala aneneri onyenga ndipo adzasocheretsa anthu ambiri. Anthu ambiri adzakhala osamvera malamulo ndipo chikondi cha anthu ambiri chidzazirala. Yesu ananenanso kuti “uthenga wabwino . . . wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”—Mateyu 24:14.

 Zimene Yesu ananena zinayamba kukwaniritsidwa mzinda wa Yerusalemu utatsala pang’ono kuwonongedwa komanso pa nthawi imene unkawonongedwa ndi Aroma. Koma kodi zimenezi zinadzakwaniritsidwanso m’tsogolo kuposa mmene zinakwaniritsidwira m’mbuyomo? Kodi inuyo mumaona umboni wotsimikizira kuti zimene Yesu ananena zikukwaniritsidwa kwambiri masiku ano?

Chinthu china chimene Yesu ananena kuti chidzakhala chizindikiro cha kukhalapo kwake, ndi kuonekera kwa ‘chinthu chonyansa komanso chowononga.’ (Mateyu 24:15) Mu 66 C.E., chinthu chonyansachi chinaonekera pamene “magulu ankhondo” a Aroma, omwe ananyamula zizindikiro za mafano komanso mbendera zawo, anazungulira mzinda wa Yerusalemu ndipo anawononga mbali zina za mpanda wa mzindawo. (Luka 21:20) Choncho “chinthu chonyansa” chinaima pa malo amene sichinkayenera kuima chifukwa Ayuda ankaona kuti ‘malowa anali oyera.’

Yesu ananenanso kuti: “Kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pa chiyambi cha dziko mpaka tsopano, ndipo sichidzachitikanso.” Mu 70 C.E., Aroma anawononga mzinda wa Yerusalemu. Kuwonongedwa kwa ‘mzinda woyera’ wa Ayuda komanso kachisi chinalidi chisautso chachikulu ndipo anthu ambiri anaphedwa. (Mateyu 4:5; 24:21) Zimene zinachitika pa nthawiyi zinali zoopsa kwambiri kuposa zinthu zonse zomwe zinachitikirapo mzindawu komanso anthu ake ndipo kupembedza kwa Ayuda kunathanso m’nthawi imeneyi. Zimenezi zikusonyeza kuti ulosi umenewu ukamadzakwaniritsidwanso m’tsogolo padzachitika zinthu zoopsa kwambiri.

TIYENERA KUKHALA NDI CHIKHULUPIRIRO M’MASIKU OTSIRIZA ANO

Pamene Yesu ankakambirana ndi atumwi ake za chizindikiro cha kukhalapo kwake monga Mfumu komanso za mapeto a dziko loipali ananenanso zinthu zina. Anawachenjeza za “onamizira kukhala Khristu ndi aneneri onyenga.” Iye ananena kuti anthu amenewa adzachita zimenezi “kuti ngati n’kotheka, adzasocheretse ngakhale osankhidwawo.” (Mateyu 24:24) Koma anthu osankhidwawo sadzasocheretsedwa. Kukhalapo kwa Khristu sikudzakhala koonekera koma anthu amene adzanamizire kuti ndi Khristu adzaonekera.

Pofotokoza zimene zidzachitike pa chisautso chachikulu chimene chidzayambe dziko la Satanali likadzatsala pang’ono kutha, Yesu ananena kuti: “Dzuwa lidzachita mdima ndipo mwezi sudzapereka kuwala kwake. Nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndipo mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka.” (Mateyu 24:29) Atumwi amene anamva zinthu zochititsa mantha zimene Yesu ananenazi, sanamvetse zimene zidzachitike koma anadziwa kuti zidzakhala zoopsa kwambiri.

Koma kodi anthu adzatani akadzaona zoopsazi? Yesu ananena kuti: “Anthu adzakomoka chifukwa cha mantha ndi kuyembekezera zimene zichitikire dziko lapansi kumene kuli anthu, pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka.” (Luka 21:26) Pamenepatu Yesu ankafotokoza za nthawi imene kudzachitike zinthu zoopsa kwambiri zimene anthu sanazionepo n’kale lonse.

N’zolimbikitsa kwambiri kuti Yesu anathandiza ophunzira ake kudziwa kuti si anthu onse amene adzalire akadzaona “Mwana wa munthu akubwera pamitambo ya kumwamba ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.” (Mateyu 24:30) Tikutero chifukwa Yesu anali atafotokoza kale kuti Mulungu adzalowererapo “chifukwa cha osankhidwawo.” (Mateyu 24:22) Ndiye kodi ophunzira okhulupirika adzatani akadzaona zinthu zimene Yesu anafotokozazi? Yesu analimbikitsa otsatira ake kuti: “Zinthu izi zikadzayamba kuchitika, mudzaimirire chilili ndi kutukula mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chikuyandikira.”—Luka 21:28.

Koma kodi ophunzira a Yesu amene adzakhale ndi moyo pa nthawi imeneyi adzadziwa bwanji kuti mapeto ayandikira? Yesu ananena fanizo la mtengo wa mkuyu. Iye anati: “Nthambi yake yanthete ikaphuka ndi kuchita masamba, mumadziwa kuti dzinja lili pafupi. Inunso chimodzimodzi, mukadzaona zinthu zonsezi, mudzadziwe kuti iye ali pafupi, ali pakhomo penipeni. Ndithu ndikukuuzani kuti m’badwo uwu sudzatha wonse kuchoka kufikira zinthu zonsezi zitachitika.”—Mateyu 24:32-34.

Choncho ophunzirawo akadzayamba kuona mbali zosiyanasiyana za chizindikirocho zikukwaniritsidwa, adzazindikire kuti mapeto ayandikira. Pofuna kuchenjeza ophunzira ake amene adzakhale ndi moyo pa nthawi imeneyo, Yesu ananena kuti:

 “Kunena za tsikulo ndi ola lake, palibe amene akudziwa, ngakhale angelo akumwamba kapenanso Mwana, koma Atate yekha. Pakuti monga mmene analili masiku a Nowa, ndi mmenenso kukhalapo kwa Mwana wa munthu kudzakhalire. M’masiku amenewo chigumula chisanafike, anthu anali kudya ndi kumwa. Amuna anali kukwatira ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m’chingalawa. Anthu ananyalanyaza zimene zinali kuchitika mpaka chigumula chinafika n’kuwaseseratu onsewo. Zidzateronso ndi kukhalapo kwa Mwana wa munthu.” (Mateyu 24:36-39) Yesu anayerekezera zimene zidzachitike pa nthawiyo ndi zimene zinachitika pa Chigumula cha m’nthawi ya Nowa chimene chinachitika padziko lonse lapansi.

Ophunzira amene anamva Yesu akunena zimenezi pamene anali pa phiri la Maolivi, mosakayikira anadziwa kufunika kokhala tcheru. Tikutero chifukwa Yesu ananenanso kuti: “Samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi kudya kwambiri, kumwa kwambiri, ndi nkhawa za moyo, kuti tsikulo lingadzakufikireni modzidzimutsa ngati msampha. Pakuti lidzafikira onse okhala pankhope ya dziko lonse lapansi. Chotero khalani maso ndipo muzipemphera mopembedzera nthawi zonse, kuti mudzathe kuthawa zinthu zonsezi zimene zikuyembekezeka kuchitika. Kutinso mudzathe kuima pamaso pa Mwana wa munthu.”—Luka 21:34-36.

Zimene Yesu ananenazi zinasonyezanso kuti zimene analosera zidzachitika kwa nthawi yaitali. Ulosiwu sunkanena za zinthu zomwe zidzachitike pa zaka zochepa kapena zimene zidzachitikire mzinda wa Yerusalemu kapena mtundu wa Ayuda okha. Iye ankanena zinthu zimene zidzachitikire anthu “onse okhala pankhope ya dziko lonse lapansi.”

Ananena kuti ophunzira ake ayenera kukhala maso, kukhala tcheru komanso kukhala okonzeka. Iye ananenanso fanizo lina pofuna kuthandiza ophunzirawo kumvetsa mfundo imeneyi. Ananena kuti: “Dziwani ichi: Ngati mwininyumba angadziwe nthawi yobwera mbala, angakhale maso ndipo sangalole kuti mbala zithyole ndi kulowa m’nyumba mwake. Pa chifukwa chimenechi, nanunso khalani okonzeka, chifukwa pa ola limene simukuliganizira, Mwana wa munthu adzabwera.”—Mateyu 24:43, 44.

Yesu ananenanso zinthu zina zomwe zinathandiza ophunzira ake kuti aziyembekezera zinthu zabwino. Iye anawauza kuti zimene ananena zikamadzakwaniritsidwa, padzakhala “kapolo” amene adzakhala tcheru komanso adzakhala akugwira ntchito. Ndiyeno Yesu anafotokoza zinthu zimene ophunzirawo akanatha kuzimvetsa. Anawauza kuti: “Ndani kwenikweni amene ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amene mbuye wake anamuika kuti aziyang’anira antchito ake apakhomo, ndi kuwapatsa chakudya pa nthawi yoyenera? Kapolo ameneyu adzakhala wodala ngati mbuye wake pobwera adzam’peza akuchita zimenezo! Ndithu ndikukuuzani, Adzamuika kuti aziyang’anira zinthu zake zonse.” Koma ngati ‘kapoloyo’ atayamba khalidwe loipa n’kuyamba kuchitira nkhanza antchito anzake, Mbuye wake “adzam’patsa chilango choopsa.”—Mateyu 24:45-51; yerekezerani ndi Luka 12:45, 46.

Komabe sikuti Yesu ankatanthauza kuti ophunzira ake ena adzayamba khalidwe loipa. Ndiye kodi pamenepa Yesu ankafuna kuti ophunzira ake amvetse mfundo iti? Iye ankafuna kuti ophunzira ake azikhala tcheru komanso kuti azigwira ntchito ndipo anathandiza ophunzira ake kumvetsa zimenezi m’fanizo lina limene ananena.