MATEYU 21:1-11, 14-17 MALIKO 11:1-11 LUKA 19:29-44 YOHANE 12:12-19

  • YESU ANALOWA MU YERUSALEMU MWAULEMERERO

  • YESU ANANENERATU KUTI YERUSALEMU ADZAWONONGEDWA

Yesu ndi ophunzira ake anachoka ku Betaniya n’kulowera ku Yerusalemu Lamlungu pa Nisani 9. Pamene ankayandikira mzinda wa Betefage, womwe unali paphiri la Maolivi, Yesu anauza ophunzira ake awiri kuti:

“Pitani m’mudzi umene mukuuonawo. Kumeneko mukapeza bulu atam’mangirira limodzi ndi mwana wake wamphongo. Mukawamasule ndi kuwabweretsa kwa ine. Wina aliyense akakakufunsani chilichonse, mukanene kuti, ‘Ambuye akuwafuna.’ Ndipo nthawi yomweyo akawatumiza kuno.”—Mateyu 21:2, 3.

Ophunzira a Yesu sanazindikire kuti zimene Yesu anawauzazo zinali zogwirizana ndi ulosi wa m’Baibulo. Patapita nthawi ophunzirawo anazindikira kuti zimene zinachitika pa nthawiyo zinakwaniritsa ulosi wa Zekariya. Zekariya analosera kuti Mfumu yomwe Mulungu analonjeza idzalowa mu Yerusalemu ‘modzichepetsa ndipo idzabwera itakwera bulu. Idzabwera itakwera nyama yokhwima, imene ndi mwana wamphongo wa bulu.’—Zekariya 9:9.

Ophunzirawo atafika ku Betefage kuti akatenge bulu wamphongoyo pamodzi ndi mayi wake, anthu amene anaima chapafupi anafunsa kuti: “Cholinga chanu n’chiyani pomasula buluyu?” (Maliko 11:5) Koma anthuwo analola ophunzirawo kutenga abuluwo atamva kuti Ambuye ndi amene ankawafuna. Ophunzirawo anayala malaya awo akunja pabulu wamkulu komanso pa mwana wake koma Yesu anakwera bulu wamng’onoyo.

Pamene Yesu ankayandikira ku Yerusalemu kunayamba kubwera anthu ambiri kuti adzamuone. Anthu ambiri anayala zovala zawo mumsewu pomwe ena anathyola nthambi za mitengo kapena “zitsamba m’minda” n’kuziyala pansi. Iwo ankafuula kuti: “M’pulumutseni! Wodalitsidwa iye wobwera m’dzina la Yehova! Wodalitsidwa ufumu ukubwerawo wa atate wathu Davide!” (Maliko 11:8-10) Afarisi amene anali pa gululo anakhumudwa ndi zimene anthuwo ankanena ndipo anauza Yesu kuti: “Mphunzitsi, adzudzuleni ophunzira anuwa.” Koma Yesu anawayankha kuti: “Ndithu ndikukuuzani, ngati awa atakhala chete, miyala ingathe kufuula.”—Luka 19:39, 40.

Yesu ataona mzinda wa Yerusalemu, anayamba kulira ndipo ananena kuti: “Iwe ukanazindikira lero zinthu zamtendere . . . koma tsopano zabisika kuti usathe kuziona.” Anthu okhala mu Yerusalemu ankayembekezera kulangidwa chifukwa chosamvera mwadala. Ponena za anthu amenewa Yesu ananeneratu kuti: “Adani ako adzamanga mpanda wazisonga kukuzungulira. Adaniwo adzakutsekereza ndi kukusautsa kuchokera kumbali zonse. Iwo adzakuwononga limodzi ndi ana ako amene ali mwa iwe. Ndipo sadzasiya mwala pamwala unzake.” (Luka 19:42-44) Zimene Yesu ananenazi zinachitikadi chifukwa mu 70 C.E., Yerusalemu anawonongedwa.

Yesu atalowa mumzinda wa Yerusalemu ‘mzinda wonse unagwedezeka. Ena anali kufunsa kuti: “Kodi ameneyu ndani?”’ Gulu la anthulo linkayankha kuti: “Ameneyu ndi mneneri Yesu, wochokera ku Nazareti, ku Galileya!” (Mateyu 21:10, 11) Anthu ena pa gulupo omwe anaona Yesu akuukitsa Lazaro ankauza anzawo zimene zinachitika. Pamenepatu Afarisiwo anachita kuoneratu kuti alemba m’madzi moti ankauzana kuti: “Dziko lonse lakhamukira kwa iye.”—Yohane 12:18, 19.

Monga mwa chizolowezi chake akapita ku Yerusalemu, Yesu anapita kukachisi kukaphunzitsa. Ali kukachisiko anachiritsa munthu wakhungu komanso wina amene anali wolumala. Koma ansembe aakulu ndi alembi anakwiya kwambiri ataona kuti Yesu wachiritsa anthuwo komanso atamva ana amene ankakuwa kuti “m’pulumutseni Mwana wa Davide!” Atsogoleri achipembedzowo anafunsa Yesu kuti: “Kodi ukumva zimene awa akunenazi?” Yesu anawayankha kuti: “Inde. Kodi simunawerenge zimenezi kuti, ‘M’kamwa mwa ana ndi mwa ana oyamwa mwaikamo mawu otamanda’?”—Mateyu 21:15, 16.

Yesu anayang’ana zinthu zomwe zinali m’kachisimo koma nthawi inali itatha kale. Choncho iye limodzi ndi atumwi ake anabwerera ku Betaniya tsiku la Nisani 10 lisanayambe. Iwo anagona ku Betaniyako usiku wa Lamlungu.