MATEYU 22:15-40 MALIKO 12:13-34 LUKA 20:20-40

  • PEREKANI ZA KAISARA KWA KAISARA

  • KODI ANTHU AMENE ADZAUKITSIDWE ADZAKWATIRA KAPENA KUKWATIWANSO?

  • MALAMULO AKULUAKULU

Atsogoleri achipembedzo anakwiya kwambiri ndi Yesu chifukwa ananena mafanizo omwe anasonyeza kuti atsogoleriwo anali anthu oipa kwambiri. Afarisi anagwirizana zoti amugwire. Iwo anapangana zoti Yesu akalankhula zinazake amugwire n’kukamupereka kwa wolamulira wachiroma moti anapatsa ndalama ena mwa ophunzira awo kuti akamugwire.—Luka 6:7.

Ophunzira a Afarisiwo anafunsa Yesu kuti: “Mphunzitsi, tikudziwa kuti mumanena ndi kuphunzitsa molondola ndipo mulibe tsankho, koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu mogwirizana ndi choonadi. Kodi n’kololeka kuti ife tizipereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?” (Luka 20:21, 22) Yesu sanapusitsike ndi funso lawo lachinyengolo. Ngati Yesu akanayankha kuti, ‘Ayi, sikololeka kupereka msonkho,’ akanaimbidwa mlandu woukira boma la Aroma. Komanso ngati akanayankha kuti, ‘Inde, muzikhoma msonkho,’ anthu omwe ankadana ndi ulamuliro wa Aroma akanaganiza kuti Yesu ali ku mbali ya Aroma ndipo akanamuukira. Ndiye kodi Yesu anawayankha bwanji?

Iye ananena kuti: “Onyenga inu! Bwanji mukundiyesa? Ndionetseni khobidi la msonkho.” Pamenepo anam’bweretsera khobidi limodzi la dinari. Ndiyeno anawafunsa kuti: “Kodi nkhope iyi ndi mawu akewa n’zandani?” Iwo anayankha kuti: “Ndi za Kaisara.” Pamenepo iye anawauza kuti: “Ndiye perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu, kwa Mulungu.”—Mateyu 22:18-21.

Anthuwo anagoma kwambiri ndi zimene Yesu anawayankha moti anasowa chonena n’kungochokapo. Ichi chinali chiyambi chabe chifukwa anthu aja  atalephera kumukola, panabweranso gulu la atsogoleri achipembedzo kudzamuyesa.

Asaduki omwe sankakhulupirira kuti anthu omwe anamwalira adzauka, anafunsa Yesu funso lokhudza za kuuka kwa akufa komanso za ukwati wa pachilamu. Iwo anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, Mose anati, ‘Ngati munthu wamwalira wopanda ana, m’bale wake ayenera kukwatira mkazi wamasiyeyo ndi kuberekera m’bale wake uja ana.’ Tsopano panali amuna 7 apachibale. Woyamba anakwatira kenako n’kumwalira. Koma popeza kuti analibe ana, mkazi uja anakwatiwa ndi m’bale wa mwamuna wake. Zinachitika chimodzimodzi kwa wachiwiri ndi wachitatu, mpaka kwa onse 7 aja.Pamapeto pake mkaziyo nayenso anamwalira. Kodi pamenepa, pouka kwa akufa, mkazi ameneyu adzakhala wa ndani popeza onse 7 anamukwatira?”—Mateyu 22:24-28.

Poyankha Asadukiwo, Yesu anagwiritsa ntchito mawu amene Mose analemba omwenso Asadukiwo ankawakhulupirira. Iye ananena kuti: “Mukulakwitsa. Kodi kulakwitsa kumeneku si chifukwa chakuti simudziwa Malemba kapena mphamvu ya Mulungu? Akadzauka kwa akufa, amuna sadzakwatira ndipo akazi sadzakwatiwa, koma adzakhala ngati angelo akumwamba. Koma zakuti akufa amaukitsidwa, kodi inu simunawerenge m’buku la Mose, m’nkhani ya chitsamba chaminga, mmene Mulungu anamuuzira kuti, ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo’? Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa. Mukulakwitsa kwambiri anthu inu.” (Maliko 12:24-27; Ekisodo 3:1-6) Gulu la anthulo linadabwa kwambiri ndi zimene Yesu anawayankha.

Yesu anasowetsa chonena Afarisi ndi Asaduki, kenako magulu awiriwa anapanga gulu limodzi ndipo anapitanso kwa Yesu kuti akamuyese. Mlembi wina pa gululo anafunsa Yesu kuti: “Mphunzitsi, kodi lamulo lalikulu kwambiri m’Chilamulo ndi liti?”—Mateyu 22:36.

Yesu anayankha kuti: “Loyamba n’lakuti, ‘Tamverani Aisiraeli inu, Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi. Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse ndi mphamvu zako zonse.’ Lachiwiri ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’ Kulibe lamulo lina lalikulu kuposa amenewa.”—Maliko 12:29-31.

Mlembiyo ananena kuti: “Mphunzitsi, mwanena bwino mogwirizana ndi choonadi, ‘Iye ndi Mmodzi, ndipo palibenso wina, koma Iye yekha.’ Kunena za kukonda Mulungu ndi mtima wonse, maganizo onse, mphamvu zonse, komanso kukonda mnzako mmene umadzikondera wekha, n’zofunika kwambiri kuposa nsembe zonse zopsereza zathunthu ndi nsembe zina.” Pamenepo Yesu, pozindikira kuti mlembiyo wayankha mwanzeru anamuuza kuti: “Iwe suli kutali ndi ufumu wa Mulungu.”—Maliko 12:32-34.

Kwa masiku atatu, kuyambira pa Nisani 9, 10 ndi 11, Yesu anakhala akuphunzitsa m’kachisi. Anthu ena anasangalala kumva zimene Yesu ankaphunzitsa ndipo m’modzi mwa anthuwo anali mlembiyu. Koma atsogoleri achipembedzo sanasangalale naye moti palibe amene “analimba mtima kumufunsanso.”