LUKA 14:7-24

  • ANAWAPHUNZITSA KUFUNIKA KOKHALA ODZICHEPETSA

  • ANAPEREKA ZIFUKWA ZOSAMVEKA ATAITANIDWA

Yesu atachiritsa munthu yemwe anali ndi matenda omwe ankamuchititsa kutupa manja ndi miyendo, anakhalabe ku nyumba kwa Mfarisi uja. Ali kunyumbako anaona anthu ena amene anaitanidwa ku chakudyacho akusankha kukhala pamalo olemekezeka. Iye anaona kuti imeneyi inali nthawi yabwino yophunzitsa anthu kufunika kokhala odzichepetsa.

Yesu ananena kuti: “Wina akakuitana kuphwando laukwati, usakhale pamalo olemekezeka kwambiri. Mwina n’kutheka kuti waitananso wina wolemekezeka kuposa iwe, ndipo amene wakuitana uja angabwere ndi wolemekezekayo kudzakuuza kuti, ‘Choka pamenepa pakhale bambo awa.’ Pamenepo udzachokapo mwamanyazi n’kukakhala kumapeto kwenikweni.”—Luka 14:8, 9.

Kenako Yesu ananena kuti: “Koma ukaitanidwa, pita ndipo ukakhale kumapeto kwenikweni, kuti munthu amene wakuitana uja akafika adzakuuze kuti, ‘Bwanawe, khala pamalo aulemuwa.’ Pamenepo udzalemekezeka pamaso pa alendo anzako onse.” Ananenanso kuti: “Pakuti aliyense wodzikweza adzatsitsidwa, ndipo wodzichepetsa adzakwezedwa.” (Luka 14:10, 11) Pamenepa Yesu ankalimbikitsa anthuwo kuti azikhala odzichepetsa.

Ndiyeno Yesu ananenanso mfundo ina yomwe inali yothandiza kwa Mfarisi amene anamuitana uja. Mfundo yake inali yoti Mfarisiyu aziganizira kwambiri za anthu amene angawaitane ku chakudya n’cholinga choti Mulungu azimukonda. Iye ananena kuti: “Ukakonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usaitane mabwenzi ako, kapena abale ako, kapena afuko lako, kapena anthu olemera omwe amakhala nawe pafupi. Mwina nthawi ina iwonso angadzakuitane ndipo kudzakhala ngati kukubwezera. Koma ukakonza phwando, uziitana anthu osauka, otsimphina, olumala, ndi akhungu. Ukatero udzakhala wodala, chifukwa alibe choti adzabweze kwa iwe. Pakuti udzabwezeredwa pa kuuka kwa anthu olungama.”—Luka 14:12-14.

Nthawi zambiri anthu amakonda kuitanira anzawo, achibale awo kapena anthu amene amakhala nawo pafupi kuti adzadye nawo chakudya ndipo Yesu sananene kuti zimenezi ndi zolakwika. Koma mfundo yake yaikulu inali yakuti, ngati munthu ataitanira chakudya anthu osauka, olumala kapena akhungu, Mulungu akhoza kumudalitsa kwambiri munthuyo. Yesu anauza Mfarisi uja kuti: “Udzabwezeredwa pa kuuka kwa anthu olungama.” Mlendo wina amene anaitanidwanso anavomereza mfundo imeneyi ndipo anati: “Wodala ndi munthu wakudya chakudya mu ufumu wa Mulungu.” (Luka 14:15) Mlendo ameneyu anaona kuti unali mwayi waukulu kudya chakudya mu Ufumu wa Mulungu koma anthu ambiri sanayamikire mwayi umenewu. Ndiyeno Yesu ananena fanizo lomwe linasonyeza kuti anthu ambiri sankaona kuti kudya ndi Mulungu ndi mwayi waukulu.

Iye ananena kuti: “Munthu wina anakonza phwando lalikulu la chakudya chamadzulo ndipo anaitana anthu ambiri. . . . Anatumiza kapolo wake kukauza oitanidwawo kuti, ‘Tiyeni, chifukwa zonse zakonzedwa tsopano.’ Koma onse mofanana anayamba kupereka zifukwa zokanira. Woyamba anamuuza kuti, ‘Ine ndagula munda, choncho ndiyenera kupita kukauona. Pepani sinditha kufika!’ Wina ananena kuti, ‘Ine ndagula ng’ombe 10 zapagoli ndipo ndikupita kukaziyesa. Pepani sinditha kufika!’ Komanso wina anati, ‘Ine ndangokwatira kumene, choncho sindingathe kubwera.’”—Luka 14:16-20.

Zifukwazi zinali zosamveka. Munthu amakaona munda kapena ng’ombe asanagule. Choncho n’zosamveka kuti azikaona zinthuzi atazigula kale. Munthu wachitatuyu sankakonzekera zokwatira. Anali atakwatira kale ndiye chimenechi sichinali chifukwa chokanira. Wokonza phwandoyo atamva zifukwazo anakwiya kwambiri ndipo anauza kapolo wakeyo kuti:

“Pita mwamsanga m’misewu ndi m’njira za mumzindawu, ukatenge anthu osauka, otsimphina, akhungu ndi olumala ndi kubwera nawo kuno.’ Patapita kanthawi kapolo uja anati, ‘Mbuyanga, zimene munalamula zachitika, komabe malo adakalipo.’ Ndiyeno mbuye uja anauza kapolo wakeyo kuti, ‘Pita m’misewu ndi malo a kumpanda, uwalimbikitse kuti abwere kuno kuti nyumba yanga idzaze. Pakuti ndikukuuzani anthu inu, Palibe ndi mmodzi yemwe mwa oitanidwa  aja amene adzalaweko chakudya changa chamadzulochi.”—Luka 14:21-24.

Zimene Yesu anafotokozazi zinasonyeza kuti Yehova Mulungu anamupatsa udindo woitana anthu kuti adzalowe mu Ufumu wakumwamba. Anthu oyamba kuitanidwa anali Ayuda omwe anali atsogoleri achipembedzo. Koma atsogoleri ambiri anakana mwayi umenewu pa nthawi yonse imene Yesu ankalalikira. Ndiyeno mwayi umenewu unaperekedwanso kwa anthu ena. Zimene Yesu ananena m’fanizo lija zinasonyeza kuti m’tsogolo padzaperekedwanso mwayi woti anthu ena alowe mu Ufumu ndipo anthu ake ndi Ayuda wamba komanso anthu omwe anatembenukira ku Chiyuda. Kenako mwayi wachitatu komanso womaliza udzaperekedwa kwa anthu amene Ayuda ankawaona kuti ndi osafunika pamaso pa Mulungu.—Machitidwe 10:28-48.

Choncho zimene Yesu anafotokozazi zinasonyeza kuti anagwirizana ndi zimene mlendo uja ananena kuti: “Wodala ndi munthu wakudya chakudya mu ufumu wa Mulungu.”